< Aroma 12 >

1 Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.
Therefore I urge you, brothers, by the mercies of God, to present your bodies a living sacrifice, holy, acceptable to God, which is your reasonable service.
2 Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro. (aiōn g165)
And do not be conformed to this world, but be transformed by the renewing of your mind, so that you may prove what is the good, well-pleasing, and perfect will of God. (aiōn g165)
3 Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.
For I say, through the grace that was given me, to everyone among you, not to think of himself more highly than he ought to think; but to think reasonably, as God has apportioned to each person a measure of faith.
4 Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana.
For even as we have many members in one body, and all the members do not have the same function,
5 Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake.
so we, who are many, are one body in Meshikha, and individually members one of another.
6 Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake.
Having gifts differing according to the grace that was given to us, if prophecy, let us prophesy according to the proportion of our faith;
7 Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse.
or service, let us give ourselves to service; or he who teaches, to his teaching;
8 Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.
or he who exhorts, to his exhorting: he who gives, let him do it with liberality; he who rules, with diligence; he who shows mercy, with cheerfulness.
9 Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino.
Let love be without hypocrisy. Abhor that which is evil. Cling to that which is good.
10 Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni.
In love of the brothers be tenderly affectionate one to another; outdo one another in showing honor;
11 Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye.
not lagging in diligence; fervent in spirit; serving the Lord;
12 Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.
rejoicing in hope; enduring in troubles; continuing steadfastly in prayer;
13 Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.
contributing to the needs of the saints; given to hospitality.
14 Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere.
Bless those who persecute you; bless, and do not curse.
15 Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.
Rejoice with those who rejoice. Weep with those who weep.
16 Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.
Be of the same mind one toward another. Do not be arrogant, but associate with the humble. Do not be wise in your own conceits.
17 Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense.
Repay no one evil for evil. Respect what is honorable in the sight of all people.
18 Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere.
If it is possible, as much as it is up to you, be at peace with all people.
19 Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye.
Do not seek revenge yourselves, beloved, but leave room for the wrath. For it is written, "Vengeance belongs to me; I will repay, says the Lord."
20 Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”
Therefore "If your enemy is hungry, feed him. If he is thirsty, give him a drink; for by doing this you will heap coals of fire on his head."
21 Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.
Do not be overcome by evil, but overcome evil with good.

< Aroma 12 >