< Aroma 10 >
1 Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.
2 Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.
3 Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu.
4 Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.
5 Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
6 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’” (ndiko, kukatsitsa Khristu)
7 “kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa). (Abyssos )
8 Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira,
9 kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
10 Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.
11 Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”
12 Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye
13 pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
14 Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?
15 Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”
16 Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?”
17 Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.
18 Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
19 Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti, “Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake. Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
20 Ndipo Yesaya molimba mtima akuti, “Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”
21 Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti, “Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga kwa anthu osandimvera ndi okanika.”