< Chivumbulutso 7 >

1 Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse.
Dann sah ich vier Engel stehen an den vier Enden der Erde, die hielten die vier Winde der Erde fest, damit kein Wind wehe über die Erde noch über das Meer noch über irgendeinen Baum.
2 Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti,
Auch sah ich einen anderen Engel aufsteigen von Sonnenaufgang her, der trug das Siegel des lebendigen Gottes, und er rief mit lauter Stimme den vier Engeln zu, die Macht empfangen hatten, die Erde und das Meer zu beschädigen,
3 “Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu.”
und sprach: "Beschädigt nicht die Erde noch das Meer noch die Bäume, bis wir die Knechte unseres Gottes versiegelt haben auf ihren Stirnen!"
4 Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.
Dann vernahm ich die Zahl der Versiegelten: es waren hundertvierundvierzigtausend aus allen Stämmen der Kinder Israels.
5 Ochokera fuko la Yuda analipo 12,000 amene analembedwa chizindikiro. Ochokera fuko la Rubeni analipo 12,000; ochokera fuko la Gadi analipo 12,000;
Aus dem Stamm Juda waren zwölftausend versiegelt, aus dem Stamm Ruben zwölftausend, aus dem Stamm Gad zwölftausend.
6 ochokera fuko la Aseri analipo 12,000; ochokera fuko la Nafutali analipo 12,000; ochokera fuko la Manase analipo 12,000;
Aus dem Stamm Asser zwölftausend, aus dem Stamm Naphtali zwölftausend, aus dem Stamm Manasse zwölftausend.
7 ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000; ochokera fuko la Levi analipo 12,000; ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;
Aus dem Stamm Simeon zwölftausend, aus dem Stamm Levi zwölftausend, aus dem Stamm Isaschar zwölftausend.
8 ochokera fuko la Zebuloni analipo 12,000; ochokera fuko la Yosefe analipo 12,000; ochokera fuko la Benjamini analipo 12,000.
Aus dem Stamm Sebulon zwölftausend, aus dem Stamm Josef zwölftausend, aus dem Stamm Benjamin waren zwölftausend versiegelt.
9 Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.
Danach sah ich eine große Schar, die niemand zählen konnte, aus allen Geschlechtern, Stämmen, Völkern und Sprachen, die stand vor dem Thron und dem Lamm. Sie waren angetan mit weißen Kleidern und trugen Palmenzweige in den Händen.
10 Ndipo ankafuwula mokweza kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu, wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa.”
Sie riefen mit lauter Stimme: / "Das Heil wird uns zuteil von unserem Gott, der auf dem Thron sitzt, und von dem Lamm."
11 “Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu.
Alle Engel standen rings um den Thron und um die Ältesten und die vier Lebewesen. Sie fielen vor dem Thron nieder auf ihr Angesicht, beteten Gott an
12 Iwo anati, “Ameni! Matamando ndi ulemerero, nzeru, mayamiko, ulemu, ulamuliro ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi, Ameni!” (aiōn g165)
und sprachen: / "Ja, so ist's. Lob, Herrlichkeit und Weisheit, Dank und Ehre, Macht und Stärke gebühren unserem Gott in alle Ewigkeit. Amen." (aiōn g165)
13 Pamenepo mmodzi wa akuluakulu aja anandifunsa kuti, “Kodi avala mikanjo yoyerawa ndani ndipo akuchokera kuti?”
Da nahm einer von den Ältesten das Wort und sprach zu mir: "Wer sind diese, die die weißen Kleider tragen, und woher sind sie gekommen?"
14 Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa.
Ich antwortete ihm: "Mein Herr, du weißt es." Da sprach er zu mir: "Diese sind gekommen aus der großen Trübsal und haben ihre Kleider in des Lammes Blut gewaschen und gebleicht.
15 Nʼchifukwa chake, “iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu; ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu adzawaphimba ndi tenti yake.
Darum stehen sie nun vor Gottes Thron und dienen ihm bei Tag und Nacht in seinem Tempel; und er, der auf dem Thron sitzt, wird sie in seinem Zelt schützen.
16 ‘Iwowa sadzamvanso njala, sadzamvanso ludzu, dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha.’
Sie wird nicht mehr hungern, nicht mehr dürsten; die Sonne und der Glutwind trifft sie nicht.
17 Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu adzakhala mʼbusa wawo. ‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’ ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’”
Denn das Lamm, das mitten vor dem Thron steht, wird sie weiden und leiten zu des Lebens Wasserquellen, und Gott wird alle Tränen aus ihren Augen wischen."

< Chivumbulutso 7 >