< Chivumbulutso 20 >

1 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. (Abyssos g12)
I vidjeh anđela: siđe s neba s ključima Bezdana i s velikim okovima u ruci. (Abyssos g12)
2 Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000.
Zgrabi Zmaja, Staru zmiju, to jest Ðavla, Sotonu, i okova ga za tisuću godina.
3 Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe. (Abyssos g12)
Baci ga u Bezdan koji nad njim zatvori i zapečati da više ne zavodi narode dok se ne navrši tisuću godina. Nakon toga ima biti odriješen za malo vremena. (Abyssos g12)
4 Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000.
I vidjeh prijestolja - onima što sjedoše na njih dano je suditi - i duše pogubljenih zbog svjedočanstva Isusova i zbog Riječi Božje i sve koji se ne pokloniše Zvijeri ni kipu njezinu te ne primiše žiga na čela svoja ni na ruke. Oni oživješe i zakraljevaše s Kristom tisuću godina.
5 (Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba.
Drugi mrtvi ne oživješe dok se ne navrši tisuću godina. To je ono prvo uskrsnuće.
6 Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.
Blažen i svet onaj tko je dionik toga prvog uskrsnuća! Nad njim druga smrt nema vlasti: oni će biti svećenici Božji i Kristovi i s njime će kraljevati tisuću godina.
7 Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ku ndende yake
A kad se navrši tisuću godina, Sotona će iz svoga zatvora biti pušten:
8 ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
izići će zavesti narode sa četiri kraja zemlje, Goga i Magoga, i skupiti ih u boj. Bit će ih kao pijeska morskoga.
9 Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa.
Skupiše se na prostrano polje zemlje i opkoliše tabor svetih i ljubljeni grad. Ali oganj siđe s neba te ih proguta.
10 Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya. (aiōn g165, Limnē Pyr g3041 g4442)
A njihov zavodnik, Ðavao, bačen bi u jezero ognjeno i sumporno, gdje se nalaze i Zvijer i Lažni prorok: ondje će se mučiti danju i noću u vijeke vjekova. (aiōn g165, Limnē Pyr g3041 g4442)
11 Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo.
I vidjeh veliko bijelo prijestolje i Onoga što sjede na nj: pred licem njegovim pobježe zemlja i nebo; ni mjesta im se više ne nađe.
12 Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku.
I vidjeh mrtve, velike i male: stoje pred prijestoljem, a knjige se otvoriše. I otvori se jedna druga knjiga, knjiga života. I mrtvi bijahu suđeni po onome što stoji napisano u knjigama, po djelima svojim.
13 Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. (Hadēs g86)
More predade svoje mrtvace, a Smrt i Podzemlje svoje: i svaki bi suđen po djelima svojim. (Hadēs g86)
14 Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. (Hadēs g86, Limnē Pyr g3041 g4442)
A Smrt i Podzemlje bili su bačeni u jezero ognjeno. Jezero ognjeno - to je druga smrt: (Hadēs g86, Limnē Pyr g3041 g4442)
15 Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto. (Limnē Pyr g3041 g4442)
tko se god ne nađe zapisan u knjizi života, bio je bačen u jezero ognjeno. (Limnē Pyr g3041 g4442)

< Chivumbulutso 20 >