< Chivumbulutso 2 >
1 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.
Skriv til Menighedens Engel i Efesus: Dette siger han, som holder de syv Stjerner i sin højre Hånd, ham, som vandrer midt imellem de syv Guldlysestager:
2 Ine ndimadziwa zochita zako, ntchito yako yowawa ndi kupirira kwako. Ine ndimadziwa kuti sungalekerere anthu oyipa amene amadzitcha atumwi pamene sichoncho, unawayesa, ndipo unawapeza kuti ndi abodza.
Jeg kender dine Gerninger og dit Arbejde og din Udholdenhed, og at du ikke kan fordrage de onde; og du prøvede dem, som kalde sig selv Apostle og ikke ere det, og du har fundet, at de ere Løgnere;
3 Iwe wapirira ndipo wakumana ndi zovuta chifukwa cha dzina langa, ndipo sunatope.
og du har Udholdenhed, og du har døjet ondt for mit Navns Skyld og er ikke bleven træt.
4 Komabe ndili ndi chotsutsana nawe: Wataya chikondi chako chapoyamba.
Men jeg har det imod dig, at du har forladt din første Kærlighed.
5 Kumbukirani kuti munagwa kuchokera patali. Lapa ndikuchita zinthu zimene unkachita poyamba. Ngati sulapa ndidzabwera ndikukuchotsera choyikapo nyale chako pamalo pake.
Kom derfor i Hu, hvorfra du er falden, og omvend dig, og gør de forrige Gerninger; men hvis ikke, da kommer jeg over dig, og jeg vil flytte din Lysestage fra dens Sted, hvis du ikke omvender dig.
6 Komabe chokomera chako ndi chakuti umadana ndi zochita za Anikolai, zimene Inenso ndimadana nazo.
Dog, dette har du, at du hader Nikolaiternes Gerninger, som også jeg hader.
7 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.
Den, som har Øre, høre, hvad Ånden siger til Menighederne! Den, som sejrer, ham vil jeg give at æde af Livets Træ, som er i Guds Paradis.
8 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Simurna kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi Woyamba ndi Wotsiriza, amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo.
Og skriv til Menighedens Engel i Smyrna: Dette siger den første og den sidste, han, som var død og blev levende:
9 Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana.
Jeg kender din Trængsel og din Fattigdom (dog, du er rig), og Bespottelsen fra dem, som kalde sig selv Jøder og ikke ere det, men ere Satans Synagoge.
10 Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
Frygt ikke, for hvad du vil komme til at lide! Se, Djævelen vil kaste nogle af eder i Fængsel, for at I skulle fristes, og I skulle have Trængsel i ti Dage. Vær tro indtil Døden, så vil jeg give dig Livets Krone
11 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.
Den, som har Øre, høre, hvad Ånden siger til Menighederne! Den, som sejrer, skal ingenlunde skades af den anden Død.
12 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Pergamo kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse.
Og skriv til Menighedens Engel i Pergamus: Dette siger han, som har det tveæggede, skarpe Sværd:
13 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.
Jeg ved, hvor du bor, der, hvor Satans Trone er; og du holder fast ved mit Navn og fornægtede ikke min Tro, i Antipas's, mit tro Vidnes Dage, han, som blev ihjelslået hos eder, der, hvor Satan bor.
14 Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo.
Men jeg har noget lidet imod dig, at du har nogle hos dig, som holde fast ved Bileams Lære, der lærte Balak at sætte Snare for Israels Børn, for at de skulde spise Afgudsofferkød og bedrive Utugt.
15 Chimodzimodzinso inuyo muli ndi ena amene amatsatira ziphunzitso za Anikolai.
Således har også du dem, som holde fast ved Nikolaiternes Lære på lignende Vis.
16 Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.
Omvend dig! Men hvis ikke, kommer jeg snart over dig og vil stride imod dem med min Munds Sværd.
17 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’”
Den, som har Øre, høre, hvad Ånden siger til Menighederne! Den, som sejrer, ham vil jeg give af den skjulte Manna, og jeg vil give ham en hvid Sten og på Stenen et nyt Navn skrevet, som ingen kender, uden den, der får det.
18 “Lembera mngelo wampingo wa ku Tiyatira kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa Mwana wa Mulungu, amene maso ake ali ngati moto woyaka ndi mapazi ake ngati chitsulo chonyezimira.
Og skriv til Menighedens Engel i Thyatira: Dette siger Guds Søn, der har Øjne som Ildslue, og hvis Fødder ere som skinnende Malm:
19 Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zanu, chikondi chanu ndi chikhulupiriro chanu, kutumikira kwanu ndi kupirira kwanu. Ndikudziwa tsopano kuti ntchito zanu ndi zabwino kuposa zoyamba zija.
Jeg kender dine Gerninger og din Kærlighed og Tro og Tjeneste og Udholdenhed, ja, dine Gerninger, de sidste flere end de første.
20 Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano.
Men jeg har imod dig, at du finder dig i Kvinden Jesabel, som kalder sig selv en Profetinde og lærer og forfører mine Tjenere til at bedrive Utugt og spise Afgudsofferkød.
21 Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna.
Og jeg har givet hende Tid til at omvende sig, men hun vil ikke omvende sig fra sin Utugt.
22 Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo.
Se, jeg kaster hende på Sygelejet og hendes Bolere i stor Trængsel, dersom de ikke omvende sig fra deres Gerninger.
23 Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.
Og hendes Børn vil jeg slå med Død, og alle Menighederne skulle kende, at jeg er den, som ransager Nyrer og Hjerter; og jeg vil give eder, hver efter eders Gerninger.
24 Tsopano ndikunena kwa enanu a ku Tiyatira, kwa inu amene simunatsate chiphunzitso cha mkaziyo ndipo simunaphunzire zimene iwo amati ndi ‘zinsinsi zonama’ za Satana. Kwa inu mawu anga ndi akuti sindikuwunjikirani malamulo ena.
Men til eder, de øvrige, som ere i Thyatira, så mange som ikke have denne Lære, fordi de ikke kende Satans Dybder, som de kalde det, til eder siger jeg: Jeg lægger ingen anden Byrde på eder.
25 Inu mungogwiritsa zimene munaphunzira basi, mpaka Ine ndidzabwere.
Kun skulle I holde fast ved det, I have, indtil jeg kommer.
26 Amene adzapambana ndi kuchita chifuniro changa mpaka kumapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu.
Og den, som sejrer, og som indtil Enden tager Vare på mine Gerninger, ham vil jeg give Mag over Hedningerne;
27 Adzayilamulira ndi ndodo yachitsulo ndipo nadzayiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi omwe ndinalandira kwa Atate anga.
og med en Jernstav skal han vogte dem, ligesom Lerkar sønderknuses, ligesom også jeg har modtaget det af min Fader;
28 Ine ndidzamupatsanso nthanda, nyenyezi yowala mʼmamawa ija.
og jeg vil give ham Morgenstjernen.
29 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.
Den, som har Øre, høre, hvad Ånden siger til Menighederne!