< Chivumbulutso 17 >
1 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri.
І прийшов один із семи анголі́в, що мають сім чаш, і говорив зо мною, ка́жучи: „Підійди, — я покажу́ тобі засу́дження великої розпусниці, що сидить над багатьма во́дами.
2 Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”
З нею розпусту чинили зе́мні царі, і вином розпусти її впивались ме́шканці землі“.
3 Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
І в дусі повів він мене на пустиню. І побачив я жінку, що сиділа на червоній звіри́ні, переповненій імена́ми богознева́жними, яка мала сім голів і десять ро́гів.
4 Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake.
А жінка була одягнена в порфіру й кармази́н, і приоздо́блена золотом і дорогоцінним камі́нням та пе́рлами. У руці своїй мала вона золоту чашу, повну гидо́ти та не́чести розпусти її.
5 Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa: BABULONI WAMKULU MAYI WA AKAZI ADAMA NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.
А на чолі́ її було написане ім'я́, таємниця: „Великий Вавилон, — мати розпусти й гидо́ти землі“.
6 Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu. Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri.
І бачив я жінку, п'яну́ від крови святих і від крови мучеників Ісусових, і, бачивши її, дивува́вся я дивом великим.
7 Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
А ангол промовив до мене: „Чого ти диву́єшся? Я скажу́ тобі таємницю жінки й звірини, яка носить її, яка має сім голів і десять ро́гів.
8 Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera. (Abyssos )
Звіри́на, яку бачив я, була — і нема, і має вийти з безо́дні — і пі́де вона на погибіль. А ме́шканці землі, що їхні імена не записані в книгу життя від закла́дин світу, дивуватися будуть, як побачать, що звіри́на була — і нема, і з'я́виться. (Abyssos )
9 “Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri.
Тут розум, що має він мудрість. Сім голів — це сім гір, що на них сидить жінка. І сім царів, —
10 Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa.
п'ять їх упало, один є, другий іще не прийшов, а як при́йде, то мусить він трохи пробути.
11 Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.
І звіри́на, що була́ — і нема, і вона — сама во́сьма й з сімох, і йде на погибіль.
12 “Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi.
А десять тих рогів, що бачив ти їх, — то десять царів, що ще не прийняли́ царства, але при́ймуть вла́ду царську́ із звіри́ною на одну годину.
13 Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho.
Вони мають одну думку, а силу та вла́ду свою віддадуть звіри́ні.
14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”
Вони воюватимуть проти Агнця та Агнець переможе їх, бо Він — „Господь над панами та Цар над царями“. А ті, хто з Ним, покликані, і вибрані, і вірні“.
15 Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo.
І говорить до мене: „Во́ди, що бачив ти їх, де сидить та розпу́сниця, то наро́ди та люди, і племе́на та язи́ки.
16 Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto.
А десять рогів, що ти бачив їх, та звіри́на, — вони знена́видять розпусницю, спусто́шать її й обнажа́ть, і з'їдять її тіло, і огнем її спалять.
17 Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.
Бо Бог дав їм до серця, щоб волю чинили Його, маючи одну думку, і щоб царство своє віддали́ звіри́ні, аж поки не ви́повняться слова́ Божі.
18 Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”
А жінка, яку ти бачив, то місто велике, що панує над царями земними“.