< Chivumbulutso 16 >

1 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!”
Maniyere il shawat melakiwotssh «Ameree! Ik'i fayo boyitse detsts shawat wanc'uwotsi datsats kuut'uwere!» etiru een k'aaro Ik'i mootse b́keshfere tshishi.
2 Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake.
Melaki shintso amt wanc'man datsats kuut'b́k'ri, s'ootso milikito boatse b́ faúwotsnat s'ootso aroosh sagadiru ashuwotsats gondonat boon kúúnit gawo boats keshbwutsi.
3 Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa.
Melaki gitlo wanc'man aats k'araats kuut'b́k'ri, aats k'aronúwere k'irts ash s'atsok'o wotb́wtsi, aats k'armanitse beyiru kash detsts keew jamwots k'irbos'uwi.
4 Mngelo wachitatu anapita natsanula mbale yake pa mitsinje ndi akasupe amadzi ndipo zinasanduka magazi.
Melaki keezlo wanc'man fokuwotsnat aats t'úúp'uwotsats kuut'b́k'ri, boowere s'ats wotbowtsi,
5 Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti, “Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo, amene mulipo ndipo munalipo;
Aats k'aratse al detsts melakiyo hank'o bíetfere tbek'i, «Fa'onat teshts S'ayinono! hank'o ni angshfetsosh nee kááw neene,
6 pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu, nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.”
Ashuwots S'ayinwotsnat nebiyiwots s'atso bokuut'tsotse boosh s'atso ni'ishi, hanuwere boosh wotgeyike, »
7 Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti, “Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.”
Wosh t'intseyirwonwere «Ee! jam falts doonzo Izar Izewero! ni angshfuwoots arikonat kaawne» etiru k'ááro tshishi.
8 Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto.
Awdl melakiyo wanc'man aawats kuut'b́k'ri, aawnwere bk'ees'on ashuwotsi bmitsish ango bish imeyi,
9 Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.
ashuwotswere een k'ees'on mis'rne, jot'anotsatse al detsts Ik'o shúútso bo c'ashi, naandrone eratsne, bínowere mangiratsne.
10 Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu.
Utsl melakiyonwere wanc'man s'ootso k'eetsats b́ kuut'i, s'ootso mengstonúwere t'aluw wotbwtsi, ashuwots bo kic'atse tuutson bo albero bo k'eetefere bo teshi,
11 Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita.
bo shodonat bo gawatse tuutson daratstso Izar Izeweri boc'ashi, bo finatsnowere naandrone eratsne.
12 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa.
Shrtl melakiwonwere wanc'o een foko Efrat'sats b́ kuut'i, aaw keshon weyiru naashúwotssh weerindo k'aniyosh fokitsi aatso tah b́gútsi.
13 Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja.
Daruwonat s'ootson nonotse, kotets nebíyo noonotsnowere gool arts keez kim shayirwots bokeshferfe t bek'i.
14 Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse.
Bowere adits keewo finitu Fo'eraw shayirwotsiye, shayiranotswere jam falts Izar Izewer eeno aawotssh wotit kes'osh ashuwotsi ikok ko'iyosh datsatsi nugus jamwotsok ametúne.
15 “Taonani, ndikubwera ngati mbala! Wodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuti asayende maliseche kuti angaonetse maliseche ake.”
«Eshe! taa úmp'etsok'o danerawon weetwe! araatson b́ woterawok'o bí aratso ashuwots bo be'awok'o k'ande'er b́ taho kordek'et asho udeke!»
16 Kenaka mizimu ija inasonkhanitsa pamodzi mafumu ku malo amene mʼChihebri amatchedwa Armagedo.
Shayirwotswere nugúswotsi Ibrayist'i noon keew keewon Armagedoni eteets beyokok boko'iyi.
17 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!”
Shawatl Ik' melakiyonwere s'awo jongats kuut'b́k'iri, Ik' mootse fa'a naashi jooratse «S'eenwtsere» etiru een wotts k'ááro b́ keshi.
18 Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri.
Awushp'alk'o, k'ááro, gúmi kááronat een wotts datsi shek'eyo wotb́wtsi, han arts een datsi shek'eyo asho datsatse bí azeron wot danake.
19 Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake.
Een kitu keezokó bkayeyi, ash naari kitúwotswere bogaahi, Ik'o eenu Babiloni gawb́dek'i, een fayi wiyini biron s'eents wanc'o b úshetwok'owere b́ k'ali.
20 Chilumba chilichonse chinathawa ndipo mapiri sanaonekenso.
Aatson gúúrts datswots t'afbowtsi, guruwotsúwere daatseratsne,
21 Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.
Ik ikon habe úúts kilo gramiyok'o mangit shetso darotse ashuwotsats b́ oot'i, een gondbek'anwere ayidek't kic'ik b́ wottsotse ashuwots gondbek'i kic'anatse tuutson Ik'o boc'ashi.

< Chivumbulutso 16 >