< Chivumbulutso 11 >
1 Ndinapatsidwa bango longa ndodo yoyezera ndipo ndinawuzidwa kuti, “Pita, kayeze Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukawerenge anthu opembedza mʼNyumbamo.
Puis on me donna un roseau semblable à un bâton, en disant: « Lève-toi et mesure le temple de Dieu, l’autel et ceux qui y adorent.
2 Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42.
Mais le parvis extérieur du temple, laisse-le en dehors et ne le mesure pas, car il a été abandonné aux Nations, et elles fouleront aux pieds la ville sainte pendant quarante-deux mois.
3 Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.”
Et je donnerai à mes deux témoins de prophétiser, revêtus de sacs, pendant mille deux cent soixante jours.
4 Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.
Ceux-ci sont les deux oliviers et les deux candélabres qui sont dressés en présence du Seigneur de la terre.
5 Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo.
Si quelqu’un veut leur nuire, un feu sort de leur bouche qui dévore leurs ennemis: c’est ainsi que doit périr quiconque voudra leur nuire.
6 Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune.
Ils ont la puissance de fermer le ciel pour empêcher la pluie de tomber durant les jours de leur prédication; et ils ont pouvoir sur les eaux pour les changer en sang, et pour frapper la terre de toutes sortes de plaies, autant de fois qu’ils le vaudront.
7 Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. (Abyssos )
Et quand ils auront achevé leur témoignage, la bête qui monte de l’abîme leur fera la guerre, les vaincra et les tuera; (Abyssos )
8 Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako.
et leurs cadavres resteront gisants sur la place de la grande ville, qui est appelée en langage figuré Sodome et Égypte, là même où leur Seigneur a été crucifié.
9 Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira.
Des hommes des divers peuples, tribus, langues et nations verront leurs cadavres étendus trois jours et demi, sans permettre qu’on leur donne la sépulture.
10 Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi.
Et les habitants de la terre se réjouiront à leur sujet; ils se livreront à l’allégresse et s’enverront des présents les uns aux autres, parce que ces deux prophètes ont fait le tourment des habitants de la terre.
11 Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu.
Mais après trois jours et demi, un esprit de vie venant de Dieu pénétra dans ces cadavres; ils se dressèrent sur leurs pieds, et une grande crainte s’empara de ceux qui les regardaient.
12 Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona.
Et l’on entendit une grande voix venant du ciel, qui leur disait: « Montez ici. » Et ils montèrent au ciel dans une nuée, à la vue de leurs ennemis.
13 Nthawi yomweyo panachitika chivomerezi choopsa mwakuti chigawo chimodzi cha magawo khumi a mzinda chinagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho, ndipo opulumukawo anachita mantha kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wakumwamba.
A cette même heure, il se fit un grand tremblement de terre; la dixième partie de la ville s’écroula, et sept mille hommes périrent dans ce tremblement de terre; les autres, saisis d’effroi, rendirent gloire au Dieu du ciel.
14 Tsoka lachiwiri lapita; koma tsoka lachitatu likubwera posachedwapa.
Le second « malheur » est passé; voici que le troisième « malheur » vient bientôt.
15 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.” (aiōn )
Et le septième ange sonna de la trompette, et l’on entendit dans le ciel des voix fortes qui disaient: « L’empire du monde a passé à notre Seigneur et à son Christ, et il régnera aux siècles des siècles. » (aiōn )
16 Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu
Alors les vingt-quatre vieillards qui sont assis devant Dieu sur leurs trônes, se prosternèrent sur leurs faces et adorèrent Dieu, en disant:
17 Iwo anati, “Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene mulipo ndipo munalipo, chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu, ndipo mwayamba kulamulira.
« Nous te rendons grâces, Seigneur Dieu tout-puissant, qui es et qui étais, de ce que tu t’es revêtu de ta grande puissance et que tu règnes.
18 A mitundu ina anapsa mtima; koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo. Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa, yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri, anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu, wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe. Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”
Les nations se sont irritées, et ta colère est venue, ainsi que le moment de juger les morts, de donner la récompense à tes serviteurs, aux prophètes, et aux saints, et à ceux qui craignent ton nom, petits et grands, et de perdre ceux qui perdent la terre. »
19 Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.
Et le sanctuaire de Dieu dans le ciel fut ouvert, et l’arche de son alliance apparut dans son sanctuaire. Et il y eut des éclairs, des bruits, des tonnerres, un tremblement de terre et une grosse grêle.