< Masalimo 99 >
1 Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke.
여호와께서 통치하시니 만민이 떨 것이요 여호와께서 그룹 사이에 좌정 하시니 땅이 요동할 것이로다
2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova; Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
여호와께서 시온에서 광대하시고 모든 민족 위에 높으시도다
3 Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri, Iye ndi woyera.
주의 크고 두려운 이름을 찬송할찌어다 그는 거룩하시도다
4 Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera; mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
왕의 능력은 공의를 사랑하는 것이라 주께서 공평을 견고히 세우시고 야곱 중에서 공과 의를 행하시나이다
5 Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mulambireni pa mapazi ake; Iye ndi woyera.
너희는 여호와 우리 하나님을 높여 그 발등상 앞에서 경배할지어다 그는 거룩하시도다
6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.
그 제사장 중에는 모세와 아론이요 그 이름을 부르는 자 중에는 사무엘이라 저희가 여호와께 간구하매 응답하셨도다
7 Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo; iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.
여호와께서 구름 기둥에서 저희에게 말씀하시니 저희가 그 주신 증거와 율례를 지켰도다
8 Inu Yehova Mulungu wathu, munawayankha iwo; Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka, ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
여호와 우리 하나님이여, 주께서는 저희에게 응답하셨고 저희 행한 대로 갚기는 하셨으나 저희를 사하신 하나님이시니이다
9 Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mumulambire pa phiri lake loyera, pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.
너희는 여호와 우리 하나님을 높이고 그 성산에서 경배할지어다 대저 여호와 우리 하나님은 거룩하시도다