< Masalimo 98 >

1 Salimo. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso.
מִזְמ֡וֹר שִׁ֤ירוּ לַֽיהוָ֨ה ׀ שִׁ֣יר חָ֭דָשׁ כִּֽי־נִפְלָא֣וֹת עָשָׂ֑ה הוֹשִֽׁיעָה־לּ֥וֹ יְ֝מִינ֗וֹ וּזְר֥וֹעַ קָדְשֽׁוֹ׃
2 Yehova waonetsa chipulumutso chake ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.
הוֹדִ֣יעַ יְ֭הוָה יְשׁוּעָת֑וֹ לְעֵינֵ֥י הַ֝גּוֹיִ֗ם גִּלָּ֥ה צִדְקָתֽוֹ׃
3 Iye wakumbukira chikondi chake ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli; malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
זָ֘כַ֤ר חַסְדּ֨וֹ ׀ וֶֽאֱֽמוּנָתוֹ֮ לְבֵ֪ית יִשְׂרָ֫אֵ֥ל רָא֥וּ כָל־אַפְסֵי־אָ֑רֶץ אֵ֝֗ת יְשׁוּעַ֥ת אֱלֹהֵֽינוּ׃
4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.
הָרִ֣יעוּ לַֽ֭יהוָה כָּל־הָאָ֑רֶץ פִּצְח֖וּ וְרַנְּנ֣וּ וְזַמֵּֽרוּ׃
5 Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze, ndi zeze ndi mawu a kuyimba,
זַמְּר֣וּ לַיהוָ֣ה בְּכִנּ֑וֹר בְּ֝כִנּ֗וֹר וְק֣וֹל זִמְרָֽה׃
6 ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.
בַּ֭חֲצֹ֣צְרוֹת וְק֣וֹל שׁוֹפָ֑ר הָ֝רִ֗יעוּ לִפְנֵ֤י ׀ הַמֶּ֬לֶךְ יְהוָֽה׃
7 Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.
יִרְעַ֣ם הַ֭יָּם וּמְלֹא֑וֹ תֵּ֝בֵ֗ל וְיֹ֣שְׁבֵי בָֽהּ׃
8 Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo, mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;
נְהָר֥וֹת יִמְחֲאוּ־כָ֑ף יַ֝֗חַד הָרִ֥ים יְרַנֵּֽנוּ׃
9 izo ziyimbe pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, ndi mitundu ya anthu mosakondera.
לִֽפְֽנֵי־יְהוָ֗ה כִּ֥י בָא֮ לִשְׁפֹּ֪ט הָ֫אָ֥רֶץ יִשְׁפֹּֽט־תֵּבֵ֥ל בְּצֶ֑דֶק וְ֝עַמִּ֗ים בְּמֵישָׁרִֽים׃

< Masalimo 98 >