< Masalimo 96 >

1 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.
請眾齊向上主歌唱新歌,普世大地請向上主謳歌!
2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
請向上主歌唱,讚美祂的聖名,一日復一日地宣揚祂的救恩。
3 Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.
請在列邦中傳述上主的光榮,請在萬民中宣揚祂的奇功。
4 Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.
因為上主偉大,應受讚美,惟祂超越眾神,可敬可畏。
5 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
萬邦的眾神盡屬虛幻,但上主卻造成了蒼天;
6 Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.
威嚴與尊榮,常在祂的面前,權能與光耀,圍繞在祂的聖壇。
7 Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
各民各族,請將光榮歸於上主,各家各戶,請將威能歸於上主。
8 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake; bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.
請將光榮歸於上主!請進入祂的庭院奉獻祭物。
9 Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.
請穿聖潔的禮服,叩拜上主;普世大地,要在祂面前顫抖!
10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.” Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe; Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.
請在萬民中高呼:上主為王!穩定寰宇,使它不再動盪,祂以正義公道治理萬邦。
11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere; nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
願諸天歡樂,願大地踴躍,願海洋及其中的一切怒號!
12 minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo. Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;
原野及其中的一切都要舞蹈,森林中的一切樹木各顯歡樂,
13 idzayimba pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lonse mwachilungamo ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.
在上主面前歡樂,因為祂己駕臨,因為祂己駕臨,要統治大地乾坤;祂要以正義審判普世人群,以祂的忠信治理天下萬民。

< Masalimo 96 >