< Masalimo 94 >

1 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango, Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
上主,您是伸冤的天主,伸冤的天主,求您顯出!
2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi; bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
審判大地的天主,請您起來!給驕傲人施以應得的禍災!
3 Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova, mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?
上主,惡人洋洋得意,要到何時?歹徒沾沾自喜,要到何時?
4 Amakhuthula mawu onyada; onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
他們大言不慚,要到何時?作惡的人自誇,要到何時?
5 Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova; amapondereza cholowa chanu.
上主,他們蹂躪您的百姓,他們磨難您的子民,
6 Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye.
屠殺寡婦與旅客,將孤兒置於死地,
7 Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.”
他們還說:上主看不見,雅各伯的天主決不管。
8 Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
民間的愚昧者!您們應該知悉,糊塗的人!您們何時才能明白?
9 Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva? Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
裝置耳朵的,難道自己聽不著?製造眼睛的,難道自己看不到?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga? Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
訓戒萬民者,難道自己不懲治?教導人類者,難道自己無知識?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu; Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.
上主認透人的思念,原來都是虛幻。
12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza, munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
上主那些受您教訓的人,守您法律者是有福的的人,
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto, mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
您叫他在患難獲享安穩,直到給惡人們掘下了陷阱。
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake; Iye sadzasiya cholowa chake.
因為上主不拒絕自己的百姓,上主不遺棄自己的人民。
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo, ndipo onse olungama mtima adzachitsata.
原來公理必歸正義的人士,心地公正的人必追求公理。
16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa? Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
誰肯奮起替我攻打行兇的人?誰肯站起替我抵抗作惡的人?
17 Yehova akanapanda kundithandiza, bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
若不是上主扶助我,我的靈魂已歸冥所。
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,” chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
我工在想說:我的腳步快要滑倒。上主,您就以您的仁慈來扶助我。
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga, chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
憂愁焦思雖然齊集我的心神,您的安慰卻舒暢了我的靈魂。
20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
若有人冒充法律,製造苦惱,不義的法庭,豈能與您相好?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
他們殘害義人的性命,判決無辜人的流血刑。
22 Koma Yehova wakhala linga langa, ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
然而上主必定作堡壘,我的天主作我避難的磐石。
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo; Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
祂必以他們罪過來報復他們;必要用他們的凶惡來消滅他們,上主我們的天主必要消滅他們。

< Masalimo 94 >