< Masalimo 93 >

1 Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
יהוה מלך גאות לבש לבש יהוה עז התאזר אף תכון תבל בל תמוט׃
2 Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; Inu ndinu wamuyaya.
נכון כסאך מאז מעולם אתה׃
3 Nyanja zakweza Inu Yehova, nyanja zakweza mawu ake; nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
נשאו נהרות יהוה נשאו נהרות קולם ישאו נהרות דכים׃
4 Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri, ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja, Yehova mmwamba ndi wamphamvu.
מקלות מים רבים אדירים משברי ים אדיר במרום יהוה׃
5 Malamulo anu Yehova ndi osasinthika; chiyero chimakongoletsa nyumba yanu mpaka muyaya.
עדתיך נאמנו מאד לביתך נאוה קדש יהוה לארך ימים׃

< Masalimo 93 >