< Masalimo 92 >

1 Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata. Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
מזמור שיר ליום השבת ב טוב להדות ליהוה ולזמר לשמך עליון
2 Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
להגיד בבקר חסדך ואמונתך בלילות
3 kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi ndi mayimbidwe abwino a zeze.
עלי-עשור ועלי-נבל עלי הגיון בכנור
4 Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.
כי שמחתני יהוה בפעלך במעשי ידיך ארנן
5 Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi!
מה-גדלו מעשיך יהוה מאד עמקו מחשבתיך
6 Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira,
איש-בער לא ידע וכסיל לא-יבין את-זאת
7 kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya.
בפרח רשעים כמו עשב ויציצו כל-פעלי און להשמדם עדי-עד
8 Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.
ואתה מרום-- לעלם יהוה
9 Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.
כי הנה איביך יהוה-- כי-הנה איביך יאבדו יתפרדו כל-פעלי און
10 Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.
ותרם כראים קרני בלתי בשמן רענן
11 Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.
ותבט עיני בשורי בקמים עלי מרעים-- תשמענה אזני
12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
צדיק כתמר יפרח כארז בלבנון ישגה
13 odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.
שתולים בבית יהוה בחצרות אלהינו יפריחו
14 Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo, adzakhala anthete ndi obiriwira,
עוד ינובון בשיבה דשנים ורעננים יהיו
15 kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama; Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”
להגיד כי-ישר יהוה צורי ולא-עלתה (עולתה) בו

< Masalimo 92 >