< Masalimo 91 >
1 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
He who is dwelling In the secret place of the Most High, In the shade of the Mighty lodgeth habitually,
2 Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimadalira.”
He is saying of Jehovah, 'My refuge, and my bulwark, my God, I trust in Him,'
3 Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje ndi ku mliri woopsa;
For He delivereth thee from the snare of a fowler, From a calamitous pestilence.
4 Adzakuphimba ndi nthenga zake, ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo; kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
With His pinion He covereth thee over, And under His wings thou dost trust, A shield and buckler [is] His truth.
5 Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku, kapena muvi wowuluka masana,
Thou art not afraid of fear by night, Of arrow that flieth by day,
6 kapena mliri umene umayenda mu mdima, kapena zowononga za pa nthawi ya masana.
Of pestilence in thick darkness that walketh, Of destruction that destroyeth at noon,
7 Anthu 1,000 atha kufa pambali pako, anthu 10,000 kudzanja lako lamanja, koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.
There fall at thy side a thousand, And a myriad at thy right hand, Unto thee it cometh not nigh.
8 Udzapenya ndi maso ako ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.
But with thine eyes thou lookest, And the reward of the wicked thou seest,
9 Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo; wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.
(For Thou, O Jehovah, [art] my refuge, ) The Most High thou madest thy habitation.
10 Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.
Evil happeneth not unto thee, And a plague cometh not near thy tent,
11 Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;
For His messengers He chargeth for thee, To keep thee in all thy ways,
12 ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala.
On the hands they bear thee up, Lest thou smite against a stone thy foot.
13 Udzapondaponda mkango ndi njoka, udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.
On lion and asp thou treadest, Thou trampest young lion and dragon.
14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
Because in Me he hath delighted, I also deliver him — I set him on high, Because he hath known My name.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha; ndidzakhala naye pa mavuto, ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
He doth call Me, and I answer him, I [am] with him in distress, I deliver him, and honour him.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali ndi kumupulumutsa.”
With length of days I satisfy him, And I cause him to look on My salvation!