< Masalimo 90 >

1 Pemphero la Mose munthu wa Mulungu. Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo pa mibado yonse.
תפלה למשה איש-האלהים אדני--מעון אתה היית לנו בדר ודר
2 Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
בטרם הרים ילדו-- ותחולל ארץ ותבל ומעולם עד-עולם אתה אל
3 Inu mumabwezera anthu ku fumbi, mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
תשב אנוש עד-דכא ותאמר שובו בני-אדם
4 Pakuti zaka 1,000 pamaso panu zili ngati tsiku limene lapita kapena ngati kamphindi ka usiku.
כי אלף שנים בעיניך-- כיום אתמול כי יעבר ואשמורה בלילה
5 Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa, iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
זרמתם שנה יהיו בבקר כחציר יחלף
6 ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano, pofika madzulo wauma ndi kufota.
בבקר יציץ וחלף לערב ימולל ויבש
7 Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu; ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
כי-כלינו באפך ובחמתך נבהלנו
8 Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu, machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
שת (שתה) עונתינו לנגדך עלמנו למאור פניך
9 Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu; timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
כי כל-ימינו פנו בעברתך כלינו שנינו כמו-הגה
10 Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70, kapena 80 ngati tili ndi mphamvu; komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa, zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.
ימי-שנותינו בהם שבעים שנה ואם בגבורת שמונים שנה-- ורהבם עמל ואון כי-גז חיש ונעפה
11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu? Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
מי-יודע עז אפך וכיראתך עברתך
12 Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
למנות ימינו כן הודע ונבא לבב חכמה
13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Achitireni chifundo atumiki anu.
שובה יהוה עד-מתי והנחם על-עבדיך
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha, kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
שבענו בבקר חסדך ונרננה ונשמחה בכל-ימינו
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa, kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
שמחנו כימות עניתנו שנות ראינו רעה
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu, kukongola kwanu kwa ana awo.
יראה אל-עבדיך פעלך והדרך על-בניהם
17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife; tikhazikitsireni ntchito ya manja athu; inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
ויהי נעם אדני אלהינו-- עלינו ומעשה ידינו כוננה עלינו ומעשה ידינו כוננהו

< Masalimo 90 >