< Masalimo 9 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a nyimbo ya “Imfa ya Mwana.” Salimo la Davide. Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse; ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.
I will praise thee, O YHWH, with my whole heart; I will shew forth all thy marvellous works.
2 Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu; Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.
I will be glad and rejoice in thee: I will sing praise to thy name, O thou most High.
3 Adani anga amathawa, iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.
When mine enemies are turned back, they shall fall and perish at thy presence.
4 Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga; Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.
For thou hast maintained my right and my cause; thou satest in the throne judging right.
5 Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa; Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.
Thou hast rebuked the heathen, thou hast destroyed the wicked, thou hast put out their name for ever and ever.
6 Chiwonongeko chosatha chagwera adani, mwafafaniza mizinda yawo; ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.
O thou enemy, destructions are come to a perpetual end: and thou hast destroyed cities; their memorial is perished with them.
7 Yehova akulamulira kwamuyaya; wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.
But YHWH shall endure for ever: he hath prepared his throne for judgment.
8 Iye adzaweruza dziko mwachilungamo; adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.
And he shall judge the world in righteousness, he shall minister judgment to the people in uprightness.
9 Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.
YHWH also will be a refuge for the oppressed, a refuge in times of trouble.
10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
And they that know thy name will put their trust in thee: for thou, YHWH, hast not forsaken them that seek thee.
11 Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni; lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
Sing praises to YHWH, which dwelleth in Zion: declare among the people his doings.
12 Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira; Iye salekerera kulira kwa ozunzika.
When he maketh inquisition for blood, he remembereth them: he forgetteth not the cry of the humble.
13 Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira! Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
Have mercy upon me, O YHWH; consider my trouble which I suffer of them that hate me, thou that liftest me up from the gates of death:
14 kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
That I may shew forth all thy praise in the gates of the daughter of Zion: I will rejoice in thy salvation.
15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba; mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
The heathen are sunk down in the pit that they made: in the net which they hid is their own foot taken.
16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. Higayoni. (Sela)
YHWH is known by the judgment which he executeth: the wicked is snared in the work of his own hands. (Higgaion, Selah)
17 Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu. (Sheol )
The wicked shall be turned into hell, and all the nations that forget Elohim. (Sheol )
18 Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.
For the needy shall not alway be forgotten: the expectation of the poor shall not perish for ever.
19 Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane; mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
Arise, O YHWH; let not man prevail: let the heathen be judged in thy sight.
20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova; mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba. (Sela)
Put them in fear, O YHWH: that the nations may know themselves to be but men. (Selah)