< Masalimo 89 >
1 Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara. Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya; ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
2 Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya, kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.
3 Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga, ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
4 ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya. Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’” (Sela)
5 Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova, kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.
6 Pakuti ndani mu mlengalenga angalingane ndi Yehova? Ndani wofanana ndi Yehova pakati pa zolengedwa zakumwamba?
7 Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.
8 Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu? Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.
9 Mumalamula nyanja ya mafunde awukali; pamene mafunde ake awundana Inu mumawakhalitsa bata.
10 Munaphwanya Rahabe monga munthu wophedwa; ndi dzanja lanu lamphamvu munabalalitsa adani anu.
11 Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.
12 Munalenga Kumpoto ndi Kummwera; Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.
13 Mkono wanu ndi wamphamvu; dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
14 Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu; chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.
15 Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu, amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.
16 Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu; amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.
17 Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.
18 Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova, Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.
19 Kale munayankhula mʼmasomphenya, kwa anthu anu okhulupirika munati, “Ndapatsa mphamvu wankhondo; ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide; ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza; zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho; anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye, ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja, dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga, Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
27 Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa; wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
28 Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya, ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
29 Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya, mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.
30 “Ngati ana ake adzataya lamulo langa ndi kusatsatira malangizo anga,
31 ngati adzaswa malamulo anga ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
32 Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo, mphulupulu zawo powakwapula.
33 Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye, kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
34 Sindidzaswa pangano langa kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
35 Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga ndipo sindidzanama kwa Davide,
36 kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
37 udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi, mboni yokhulupirika mʼmitambo. (Sela)
38 “Koma tsopano Inu mwamukana, mwamutaya, mwamukwiyira kwambiri wodzozedwa wanu.
39 Mwakana pangano ndi mtumiki wanu ndipo mwadetsa mʼfumbi chipewa chake chaufumu.
40 Inu mwagumula makoma ake onse ndipo mwasandutsa bwinja malinga ake.
41 Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake; iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake.
42 Mwakweza dzanja lamanja la adani ake; mwachititsa kuti adani ake akondwere.
43 Mwabunthitsa lupanga lake, simunamuthandize pa nkhondo.
44 Inu mwathetsa kukongola kwa ulemerero wake ndipo mwagwetsa pansi mpando wake waufumu.
45 Mwachepetsa masiku a unyamata wake; mwamuphimba ndi chofunda chochititsa manyazi. (Sela)
46 “Mpaka liti Yehova? Kodi mudzadzibisa mpaka kalekale? Mpaka liti ukali wanu udzayaka ngati moto?
47 Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa pakuti munalenga kwachabe anthu onse!
48 Kodi ndi munthu uti angakhale ndi moyo ndi kusaona imfa? Kapena kudzipulumutsa yekha ku mphamvu ya manda? (Sela) (Sheol )
49 Inu Ambuye kodi chili kuti chikondi chanu chachikulu choyamba chija, chimene mwa kukhulupirika kwanu munalumbira kwa Davide?
50 Kumbukirani, Ambuye momwe mtumiki wanu wanyozedwera, momwe ndakhalira ndi kusunga mu mtima mwanga mawu a pangano a anthu a mitundu yonse,
51 mawu achipongwe amene adani anu akhala akunyoza, Inu Yehova, ndi mawu amene akhala akunyoza mayendedwe onse a wodzozedwa wanu.
52 “Matamando akhale kwa Yehova mpaka muyaya!”