< Masalimo 88 >
1 Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara. Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.
2 Pemphero langa lifike pamaso panu; tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.
3 Pakuti ndili ndi mavuto ambiri ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda. (Sheol )
4 Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje; ndine munthu wopanda mphamvu.
5 Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa, monga ophedwa amene agona mʼmanda, amene Inu simuwakumbukiranso, amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.
6 Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni, mʼmalo akuya a mdima waukulu.
7 Ukali wanu ukundipsinja kwambiri, mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse. (Sela)
8 Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo. Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;
9 maso anga ada ndi chisoni. Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse; ndimakweza manja anga kwa Inu.
10 Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa? Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu? (Sela)
11 Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda, za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?
12 Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima, kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?
13 Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo; mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.
14 Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana ndi kundibisira nkhope yanu?
15 Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa; ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.
16 Ukali wanu wandimiza; zoopsa zanu zandiwononga.
17 Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula; zandimiza kwathunthu.
18 Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga; mdima ndiye bwenzi langa lenileni.