< Masalimo 87 >

1 Salimo la Ana a Kora. Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
לבני-קרח מזמור שיר יסודתו בהררי-קדש
2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
אהב יהוה שערי ציון-- מכל משכנות יעקב
3 Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: (Sela)
נכבדות מדבר בך-- עיר האלהים סלה
4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’”
אזכיר רהב ובבל-- לידעי הנה פלשת וצר עם-כוש זה ילד-שם
5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
ולציון יאמר-- איש ואיש ילד-בה והוא יכוננה עליון
6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” (Sela)
יהוה--יספר בכתוב עמים זה ילד-שם סלה
7 Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”
ושרים כחללים-- כל-מעיני בך

< Masalimo 87 >