< Masalimo 85 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Yehova munakomera mtima dziko lanu; munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
לַמְנַצֵּחַ ׀ לִבְנֵי־קֹרַח מִזְמֽוֹר׃ רָצִיתָ יְהֹוָה אַרְצֶךָ שַׁבְתָּ (שבות) [שְׁבִית] יַעֲקֹֽב׃
2 Munakhululukira mphulupulu za anthu anu ndi kuphimba machimo awo onse. (Sela)
נָשָׂאתָ עֲוֺן עַמֶּךָ כִּסִּיתָ כׇל־חַטָּאתָם סֶֽלָה׃
3 Munayika pambali ukali wanu wonse ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.
אָסַפְתָּ כׇל־עֶבְרָתֶךָ הֱשִׁיבוֹתָ מֵחֲרוֹן אַפֶּֽךָ׃
4 Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
שׁוּבֵנוּ אֱלֹהֵי יִשְׁעֵנוּ וְהָפֵר כַּעַסְךָ עִמָּֽנוּ׃
5 Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?
הַלְעוֹלָם תֶּאֱנַף־בָּנוּ תִּמְשֹׁךְ אַפְּךָ לְדֹר וָדֹֽר׃
6 Kodi simudzatitsitsimutsanso, kuti anthu anu asangalale mwa Inu?
הֲֽלֹא־אַתָּה תָּשׁוּב תְּחַיֵּנוּ וְעַמְּךָ יִשְׂמְחוּ־בָֽךְ׃
7 Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova, ndipo tipatseni chipulumutso chanu.
הַרְאֵנוּ יְהֹוָה חַסְדֶּךָ וְיֶשְׁעֲךָ תִּתֶּן־לָֽנוּ׃
8 Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
אֶשְׁמְעָה מַה־יְדַבֵּר הָאֵל ׀ יְהֹוָה כִּי ׀ יְדַבֵּר שָׁלוֹם אֶל־עַמּוֹ וְאֶל־חֲסִידָיו וְאַל־יָשׁוּבוּ לְכִסְלָֽה׃
9 Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye, kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
אַךְ קָרוֹב לִירֵאָיו יִשְׁעוֹ לִשְׁכֹּן כָּבוֹד בְּאַרְצֵֽנוּ׃
10 Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi; chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
חֶסֶד־וֶאֱמֶת נִפְגָּשׁוּ צֶדֶק וְשָׁלוֹם נָשָֽׁקוּ׃
11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi, ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
אֱמֶת מֵאֶרֶץ תִּצְמָח וְצֶדֶק מִשָּׁמַיִם נִשְׁקָֽף׃
12 Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino, ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
גַּם־יְהֹוָה יִתֵּן הַטּוֹב וְאַרְצֵנוּ תִּתֵּן יְבוּלָֽהּ׃
13 Wolungama amapita patsogolo pake ndi kukonza njira za mapazi ake.
צֶדֶק לְפָנָיו יְהַלֵּךְ וְיָשֵׂם לְדֶרֶךְ פְּעָמָֽיו׃

< Masalimo 85 >