< Masalimo 84 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora. Malo anu okhalamo ndi okomadi, Inu Yehova Wamphamvuzonse!
למנצח על הגתית לבני קרח מזמור מה ידידות משכנותיך יהוה צבאות׃
2 Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufuna mabwalo a Yehova; Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira Mulungu wamoyo.
נכספה וגם כלתה נפשי לחצרות יהוה לבי ובשרי ירננו אל אל חי׃
3 Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
גם צפור מצאה בית ודרור קן לה אשר שתה אפרחיה את מזבחותיך יהוה צבאות מלכי ואלהי׃
4 Odala amene amakhala mʼNyumba yanu; nthawi zonse amakutamandani. (Sela)
אשרי יושבי ביתך עוד יהללוך סלה׃
5 Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu, mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
אשרי אדם עוז לו בך מסלות בלבבם׃
6 Pamene akudutsa chigwa cha Baka, amachisandutsa malo a akasupe; mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
עברי בעמק הבכא מעין ישיתוהו גם ברכות יעטה מורה׃
7 Iwo amanka nakulirakulira mphamvu mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.
ילכו מחיל אל חיל יראה אל אלהים בציון׃
8 Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse; mvereni Inu Mulungu wa Yakobo. (Sela)
יהוה אלהים צבאות שמעה תפלתי האזינה אלהי יעקב סלה׃
9 Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu; yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.
מגננו ראה אלהים והבט פני משיחך׃
10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
כי טוב יום בחצריך מאלף בחרתי הסתופף בבית אלהי מדור באהלי רשע׃
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.
כי שמש ומגן יהוה אלהים חן וכבוד יתן יהוה לא ימנע טוב להלכים בתמים׃
12 Inu Yehova Wamphamvuzonse, wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.
יהוה צבאות אשרי אדם בטח בך׃

< Masalimo 84 >