< Masalimo 83 >

1 Nyimbo. Salimo la Asafu. Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu.
Canto. Salmo. Di Asaf. Dio, non darti riposo, non restare muto e inerte, o Dio.
2 Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo.
Vedi: i tuoi avversari fremono e i tuoi nemici alzano la testa.
3 Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.
Contro il tuo popolo ordiscono trame e congiurano contro i tuoi protetti.
4 Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”
Hanno detto: «Venite, cancelliamoli come popolo e più non si ricordi il nome di Israele».
5 Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:
Hanno tramato insieme concordi, contro di te hanno concluso un'alleanza;
6 Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri,
le tende di Edom e gli Ismaeliti, Moab e gli Agareni,
7 Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.
Gebal, Ammon e Amalek la Palestina con gli abitanti di Tiro.
8 Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. (Sela)
Anche Assur è loro alleato e ai figli di Lot presta man forte.
9 Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.
Trattali come Madian e Sisara, come Iabin al torrente di Kison:
10 Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala.
essi furono distrutti a Endor, diventarono concime per la terra.
11 Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,
Rendi i loro principi come Oreb e Zeb, e come Zebee e Sàlmana tutti i loro capi;
12 amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.”
essi dicevano: «I pascoli di Dio conquistiamoli per noi».
13 Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.
Mio Dio, rendili come turbine, come pula dispersa dal vento.
14 Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri,
Come il fuoco che brucia il bosco e come la fiamma che divora i monti,
15 kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.
così tu inseguili con la tua bufera e sconvolgili con il tuo uragano.
16 Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.
Copri di vergogna i loro volti perché cerchino il tuo nome, Signore.
17 Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse; awonongeke mwa manyazi.
Restino confusi e turbati per sempre, siano umiliati, periscano;
18 Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.
sappiano che tu hai nome «Signore», tu solo sei l'Altissimo su tutta la terra.

< Masalimo 83 >