< Masalimo 82 >

1 Salimo la Asafu. Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.”
A Psalm of Asaph. God has stood in the synagogue of gods, but, in their midst, he decides between gods.
2 “Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa?
How long will you judge unjustly and favor the faces of sinners?
3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
Judge for the indigent and the orphan. Do justice to the humble and the poor.
4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.
Rescue the poor, and free the needy from the hand of the sinner.
5 “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
They did not know and did not understand. They wander in darkness. All the foundations of the earth will be moved.
6 “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’
I said: You are gods, and all of you are sons of the Most High.
7 Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”
But you will die like men, and you will fall just like one of the princes.
8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.
Rise up, O God. Judge the earth. For you will inherit it with all the nations.

< Masalimo 82 >