< Masalimo 81 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu. Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu; Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!
למנצח על הגתית לאסף הרנינו לאלהים עוזנו הריעו לאלהי יעקב׃
2 Yambani nyimbo, imbani tambolini imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.
שאו זמרה ותנו תף כנור נעים עם נבל׃
3 Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;
תקעו בחדש שופר בכסה ליום חגנו׃
4 ili ndi lamulo kwa Israeli, langizo la Mulungu wa Yakobo.
כי חק לישראל הוא משפט לאלהי יעקב׃
5 Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.
עדות ביהוסף שמו בצאתו על ארץ מצרים שפת לא ידעתי אשמע׃
6 Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo; Manja awo anamasulidwa mʼdengu.
הסירותי מסבל שכמו כפיו מדוד תעברנה׃
7 Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. (Sela)
בצרה קראת ואחלצך אענך בסתר רעם אבחנך על מי מריבה סלה׃
8 “Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!
שמע עמי ואעידה בך ישראל אם תשמע לי׃
9 Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu; musadzagwadire mulungu wina.
לא יהיה בך אל זר ולא תשתחוה לאל נכר׃
10 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto. Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.
אנכי יהוה אלהיך המעלך מארץ מצרים הרחב פיך ואמלאהו׃
11 “Koma anthu anga sanandimvere; Israeli sanandigonjere.
ולא שמע עמי לקולי וישראל לא אבה לי׃
12 Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo kuti atsate zimene ankafuna.
ואשלחהו בשרירות לבם ילכו במועצותיהם׃
13 “Anthu anga akanangondimvera, Israeli akanatsatira njira zanga,
לו עמי שמע לי ישראל בדרכי יהלכו׃
14 nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!
כמעט אויביהם אכניע ועל צריהם אשיב ידי׃
15 Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.
משנאי יהוה יכחשו לו ויהי עתם לעולם׃
16 Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri; ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”
ויאכילהו מחלב חטה ומצור דבש אשביעך׃

< Masalimo 81 >