< Masalimo 80 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu. Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli, Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa; Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
למנצח אל ששנים עדות לאסף מזמור רעה ישראל האזינה נהג כצאן יוסף ישב הכרובים הופיעה׃
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase. Utsani mphamvu yanu; bwerani ndi kutipulumutsa.
לפני אפרים ובנימן ומנשה עוררה את גבורתך ולכה לישעתה לנו׃
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu; nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.
אלהים השיבנו והאר פניך ונושעה׃
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse, mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
יהוה אלהים צבאות עד מתי עשנת בתפלת עמך׃
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi; mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
האכלתם לחם דמעה ותשקמו בדמעות שליש׃
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu, ndipo adani athu akutinyoza.
תשימנו מדון לשכנינו ואיבינו ילעגו למו׃
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse, nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.
אלהים צבאות השיבנו והאר פניך ונושעה׃
8 Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto; munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.
גפן ממצרים תסיע תגרש גוים ותטעה׃
9 Munawulimira munda wamphesawo, ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
פנית לפניה ותשרש שרשיה ותמלא ארץ׃
10 Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake, mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.
כסו הרים צלה וענפיה ארזי אל׃
11 Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja, mphukira zake mpaka ku mtsinje.
תשלח קצירה עד ים ואל נהר יונקותיה׃
12 Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?
למה פרצת גדריה וארוה כל עברי דרך׃
13 Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga ndipo zirombo za mthengo zimawudya.
יכרסמנה חזיר מיער וזיז שדי ירענה׃
14 Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse! Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone! Uyangʼanireni mpesa umenewu,
אלהים צבאות שוב נא הבט משמים וראה ופקד גפן זאת׃
15 muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala, mwana amene inu munamukuza nokha.
וכנה אשר נטעה ימינך ועל בן אמצתה לך׃
16 Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto; pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.
שרפה באש כסוחה מגערת פניך יאבדו׃
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja, mwana wa munthu amene mwalera nokha.
תהי ידך על איש ימינך על בן אדם אמצת לך׃
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu; titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.
ולא נסוג ממך תחינו ובשמך נקרא׃
19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.
יהוה אלהים צבאות השיבנו האר פניך ונושעה׃

< Masalimo 80 >