< Masalimo 8 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide. Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.
For the Chief Musician; on an instrument of Gath. A Psalm by David. LORD, our Lord, how majestic is your name in all the earth! You have set your glory above the heavens!
2 Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda, Inu mwakhazikitsa mphamvu chifukwa cha adani anu, kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
From the lips of babes and infants you have established strength, because of your adversaries, that you might silence the enemy and the avenger.
3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,
When I consider your heavens, the work of your fingers, the moon and the stars, which you have ordained,
4 munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira, ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
what is man, that you think of him? What is the son of man, that you care for him?
5 Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
For you have made him a little lower than the angels, and crowned him with glory and honour.
6 Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu; munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
You make him ruler over the works of your hands. You have put all things under his feet:
7 nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi ndi nyama zakuthengo,
All sheep and cattle, yes, and the animals of the field,
8 mbalame zamlengalenga ndi nsomba zamʼnyanja zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.
the birds of the sky, the fish of the sea, and whatever passes through the paths of the seas.
9 Inu Yehova, Ambuye athu, dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
LORD, our Lord, how majestic is your name in all the earth!

< Masalimo 8 >