< Masalimo 79 >

1 Salimo la Asafu. Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu; ayipitsa Nyumba yanu yoyera, asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.
מזמור לאסף אלהים באו גוים בנחלתך טמאו את היכל קדשך שמו את ירושלם לעיים׃
2 Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya, matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi.
נתנו את נבלת עבדיך מאכל לעוף השמים בשר חסידיך לחיתו ארץ׃
3 Akhetsa magazi monga madzi kuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa.
שפכו דמם כמים סביבות ירושלם ואין קובר׃
4 Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu, choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira.
היינו חרפה לשכנינו לעג וקלס לסביבותינו׃
5 Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya? Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?
עד מה יהוה תאנף לנצח תבער כמו אש קנאתך׃
6 Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina amene sakudziwani Inu, pa maufumu amene sayitana pa dzina lanu;
שפך חמתך אל הגוים אשר לא ידעוך ועל ממלכות אשר בשמך לא קראו׃
7 pakuti iwo ameza Yakobo ndi kuwononga dziko lawo.
כי אכל את יעקב ואת נוהו השמו׃
8 Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe, pakuti tili ndi chosowa chachikulu.
אל תזכר לנו עונת ראשנים מהר יקדמונו רחמיך כי דלונו מאד׃
9 Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu.
עזרנו אלהי ישענו על דבר כבוד שמך והצילנו וכפר על חטאתינו למען שמך׃
10 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti, “Ali kuti Mulungu wawo?” Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.
למה יאמרו הגוים איה אלהיהם יודע בגיים לעינינו נקמת דם עבדיך השפוך׃
11 Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu; ndi mphamvu ya dzanja lanu muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe.
תבוא לפניך אנקת אסיר כגדל זרועך הותר בני תמותה׃
12 Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.
והשב לשכנינו שבעתים אל חיקם חרפתם אשר חרפוך אדני׃
13 Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu, tidzakutamandani kwamuyaya, kuchokera mʼbado ndi mʼbado tidzafotokoza za matamando anu.
ואנחנו עמך וצאן מרעיתך נודה לך לעולם לדר ודר נספר תהלתך׃

< Masalimo 79 >