< Masalimo 78 >
1 Ndakatulo ya Asafu. Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa; mvetserani mawu a pakamwa panga.
2 Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo, ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
3 zimene tinazimva ndi kuzidziwa, zimene makolo athu anatiwuza.
4 Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
5 Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli, zimene analamulira makolo athu kuphunzitsa ana awo,
6 kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa, ngakhale ana amene sanabadwe, ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
7 Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu ndipo sadzayiwala ntchito zake koma adzasunga malamulo ake.
8 Iwo asadzakhale monga makolo awo, mʼbado wosamvera ndi wowukira, umene mitima yake inali yosamvera Mulungu, umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.
9 Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta, anathawabe pa nthawi ya nkhondo;
10 iwo sanasunge pangano la Mulungu ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.
11 Anayiwala zimene Iye anachita, zozizwitsa zimene anawaonetsa.
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona, mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo, Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.
17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye, kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 Ananyoza Mulungu mwadala pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti, “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 Iye atamenya thanthwe madzi anatuluka, ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi. Koma iye angatipatsenso ife chakudya? Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
21 Yehova atawamva anakwiya kwambiri; moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo, ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,
22 pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu kapena kudalira chipulumutso chake.
23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
24 anagwetsa mana kuti anthu adye, anawapatsa tirigu wakumwamba.
25 Anthu anadya buledi wa angelo, Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba, ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.
27 Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi, mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
28 Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo, kuzungulira matenti awo onse.
29 Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.
30 Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho, chakudya chili mʼkamwa mwawobe,
31 mkwiyo wa Mulungu unawayakira; Iye anapha amphamvu onse pakati pawo, kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.
32 Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa; ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.
33 Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya. Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.
34 Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo; iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.
35 Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo, kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.
36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo, kumunamiza ndi malilime awo;
37 Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye, iwo sanakhulupirike ku pangano lake.
38 Komabe Iye anali wachifundo; anakhululukira mphulupulu zawo ndipo sanawawononge. Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wake ndipo sanawutse ukali wake wonse.
39 Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe, mphepo yopita imene sibwereranso.
40 Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu ndi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu!
41 Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu; ankamuputa Woyera wa Israeli.
42 Sanakumbukire mphamvu zake, tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza,
43 tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto, zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.
44 Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi; Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo.
45 Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga, ndiponso achule amene anawasakaza.
46 Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala, zokolola zawo kwa dzombe.
47 Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala ndiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu.
48 Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala, zoweta zawo ku zingʼaningʼani.
49 Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo, anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
50 Analolera kukwiya, sanawapulumutse ku imfa koma anawapereka ku mliri.
51 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu
52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto; anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha koma nyanja inamiza adani awo.
54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo; Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.
56 Koma iwo anayesa Mulungu ndi kuwukira Wammwambamwamba; sanasunge malamulo ake.
57 Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo, anapotoka monga uta wosakhulupirika.
58 Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano; anawutsa nsanje yake ndi mafano awo.
59 Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri; Iye anakana Israeli kwathunthu.
60 Anasiya nyumba ya ku Silo, tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.
61 Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo, ulemerero wake mʼmanja mwa adani.
62 Anapereka anthu ake ku lupanga; anakwiya kwambiri ndi cholowa chake.
63 Moto unanyeketsa anyamata awo, ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati;
64 ansembe awo anaphedwa ndi lupanga, ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira.
65 Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo.
66 Iye anathamangitsa adani ake; anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.
67 Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe, sanasankhe fuko la Efereimu;
68 Koma anasankha fuko la Yuda, phiri la Ziyoni limene analikonda.
69 Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda, dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.
70 Anasankha Davide mtumiki wake ndi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa;
71 kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo, wa Israeli cholowa chake.
72 Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama; ndi manja aluso anawatsogolera.