< Masalimo 77 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu. Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo; ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
To the chief Musician, to Jeduthun, A Psalm of Asaph. I cried unto God with my voice, [even] unto God with my voice; and he gave ear unto me.
2 Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye; usiku ndinatambasula manja mosalekeza ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.
In the day of my trouble I sought the Lord: my sore ran in the night, and ceased not: my soul refused to be comforted.
3 Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula; ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka. (Sela)
I remembered God, and was troubled: I complained, and my spirit was overwhelmed. (Selah)
4 Munagwira zikope zanga kuti ndisagone ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
Thou holdest mine eyes waking: I am so troubled that I cannot speak.
5 Ndinaganizira za masiku akale, zaka zamakedzana;
I have considered the days of old, the years of ancient times.
6 Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku. Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,
I call to remembrance my song in the night: I commune with mine own heart: and my spirit made diligent search.
7 “Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya? Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
Will the Lord cast off for ever? and will he be favourable no more?
8 Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu? Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
Is his mercy clean gone for ever? doth [his] promise fail for evermore?
9 Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima? Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”
Hath God forgotten to be gracious? hath he in anger shut up his tender mercies? (Selah)
10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso: zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
And I said, This [is] my infirmity: [but I will remember] the years of the right hand of the most High.
11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova; Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
I will remember the works of the LORD: surely I will remember thy wonders of old.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”
I will meditate also of all thy work, and talk of thy doings.
13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera. Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
Thy way, O God, [is] in the sanctuary: who [is so] great a God as [our] God?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa; Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
Thou [art] the God that doest wonders: thou hast declared thy strength among the people.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu, zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe. (Sela)
Thou hast with [thine] arm redeemed thy people, the sons of Jacob and Joseph. (Selah)
16 Madzi anakuonani Mulungu, madzi anakuonani ndipo anachita mantha; nyanja yozama inakomoka.
The waters saw thee, O God, the waters saw thee; they were afraid: the depths also were troubled.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi, mu mlengalenga munamveka mabingu; mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
The clouds poured out water: the skies sent out a sound: thine arrows also went abroad.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu, mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
The voice of thy thunder [was] in the heaven: the lightnings lightened the world: the earth trembled and shook.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja, njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu, ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.
Thy way [is] in the sea, and thy path in the great waters, and thy footsteps are not known.
20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.
Thou leddest thy people like a flock by the hand of Moses and Aaron.