< Masalimo 76 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu. Mulungu amadziwika mu Yuda; dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.
למנצח בנגינת מזמור לאסף שיר ב נודע ביהודה אלהים בישראל גדול שמו
2 Tenti yake ili mu Salemu, malo ake okhalamo mu Ziyoni.
ויהי בשלם סוכו ומעונתו בציון
3 Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. (Sela)
שמה שבר רשפי-קשת מגן וחרב ומלחמה סלה
4 Wolemekezeka ndinu, wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.
נאור אתה אדיר-- מהררי-טרף
5 Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma, Iwowo amagona tulo tawo totsiriza; palibe mmodzi wamphamvu amene angatukule manja ake.
אשתוללו אבירי לב-- נמו שנתם ולא-מצאו כל-אנשי-חיל ידיהם
6 Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo, kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.
מגערתך אלהי יעקב נרדם ורכב וסוס
7 Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?
אתה נורא אתה--ומי-יעמד לפניך מאז אפך
8 Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo, ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,
משמים השמעת דין ארץ יראה ושקטה
9 pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze, kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko. (Sela)
בקום-למשפט אלהים-- להושיע כל-ענוי-ארץ סלה
10 Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.
כי-חמת אדם תודך שארית חמת תחגר
11 Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa.
נדרו ושלמו ליהוה אלהיכם כל-סביביו--יבילו שי למורא
12 Iye amaswa mzimu wa olamulira; amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.
יבצר רוח נגידים נורא למלכי-ארץ

< Masalimo 76 >