< Masalimo 75 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
[For the Chief Musician. To the tune of "Do Not Destroy." A Psalm by Asaph. A song.] We give thanks to you, God. We give thanks, for your Name is near. Men tell about your wondrous works.
2 Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
When I choose the appointed time, I will judge blamelessly.
3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. (Sela)
The earth and all its inhabitants quake. I firmly hold its pillars. (Selah)
4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
I said to the arrogant, "Do not boast." I said to the wicked, "Do not lift up the horn.
5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’”
Do not lift up your horn on high. Do not speak with a stiff neck."
6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu.
For neither from the east, nor from the west, nor yet from the south, comes exaltation.
7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
But God is the judge. He puts down one, and lifts up another.
8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.
For in the hand of the LORD there is a cup, full of foaming wine mixed with spices. He pours it out. Indeed the wicked of the earth drink and drink it to its very dregs.
9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
But I will declare this forever: I will sing praises to the God of Jacob.
10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.
I will cut off all the horns of the wicked, but the horns of the righteous shall be lifted up.

< Masalimo 75 >