< Masalimo 74 >

1 Ndakatulo ya Asafu. Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
Mungu, kwa nini umetukataa milele? Kwa nini hasira yako inawaka dhidi ya kondoo wa malisho yako?
2 Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale, fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola, phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
Wafikilie watu wako, ambao uliwanunua siku nyingi zilizopita, kabila ambalo wewe umelikomboa liwe urithi wako, na Milima Sayuni, mahali uishipo.
3 Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.
Uje utazame uharibifu kamili, uharibifu ambao umefanywa na adui mahali patakatifu.
4 Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe; anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
Washindani wako walivamia katikati ya mahali pako maalumu; walipandisha bendera zao za vita.
5 Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo kuti adule mitengo mʼnkhalango.
Walipakatakata kwa shoka kama katika msitu mnene.
6 Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo zonse zimene tinapachika.
Walipaharibu na kuvunja sanaa zilizonakshiwa zote; walizivunja kwa shoka na nyundo.
7 Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi; anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
Walipachoma patakatifu pako; walipanajisi mahari unapoishi, wakigongagonga kwenye ardhi.
8 Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.” Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
Walisema mioyoni mwao, “Tutawaharibu wote.” Walichoma sehemu zako zote za kukutania katika nchi.
9 Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
Sisi hatuoni tena ishara; hakuna tena nabii, na hakuna yeyote miongoni mwetu ajuaye haya yatadumu kwa muda gani.
10 Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu? Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
Mpaka lini, Mungu, adui atakurushia wewe matusi? Je, atalitukana jina lako milele?
11 Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!
Kwa nini umerudisha nyuma mkono wako, mkono wako wa kuume? Utoe mkono wako kwenye mavazi yako na uwaangamize.
12 Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale; Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
Lakini Mungu amekuwa mfalme wangu tangu enzi, akileta wokovu tuniani.
13 Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu; munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
Wewe uliigawa bahari; ulishambulia vichwa vya majitu ya kutisha baharini majini.
14 Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
Wewe ulishambulia vichwa vya lewiathani; na kumfanya awe chakula cha viumbe hai jangwani.
15 Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje, munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
Ulizifungulia chemchem na vijito; uliikausha mito itiririkayo.
16 Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso; Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
Mchana ni wako, na usiku ni wako pia; uliweka jua na mwezi mahari pake.
17 Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi; munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
Umeiweka mipaka ya nchi; umeumba majira ya joto na majira ya baridi.
18 Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova, momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
Kumbula vile adui alivyo vurumisha matusi kwako, Yahwe, na kwamba watu wapumbavu wamelitukana jina lako.
19 Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo; nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
Usimtoe njiwa afe kwa mnyama wa porini. Usiusahau milele uhai wa watu wako walio onewa.
20 Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
Kumbuka agano lako, maana majimbo ya giza ya nchi yamejaa maeneo ya vurugu.
21 Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi; osauka ndi osowa atamande dzina lanu.
Usiwaache walioonewa warudishwe kwa aibu; uwaache maskini na walioonewa walisifu jina lako.
22 Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu; kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
Inuka Mungu, itetee heshima yako; kumbuka wajinga wanavyokutukana machana kutwa.
23 Musalekerere phokoso la otsutsana nanu, chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.
Usisahau sauti ya adui zako au kelele za wale wanaoendelea kukuchafua.

< Masalimo 74 >