< Masalimo 72 >

1 Salimo la Solomoni. Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo, Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
לשלמה אלהים--משפטיך למלך תן וצדקתך לבן-מלך
2 Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo, anthu anu ozunzika mosakondera.
ידין עמך בצדק וענייך במשפט
3 Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu, timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
ישאו הרים שלום לעם וגבעות בצדקה
4 Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo.
ישפט עניי-עם--יושיע לבני אביון וידכא עושק
5 Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse, nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
ייראוך עם-שמש ולפני ירח דור דורים
6 Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
ירד כמטר על-גז כרביבים זרזיף ארץ
7 Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika; chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.
יפרח-בימיו צדיק ורב שלום עד-בלי ירח
8 Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
וירד מים עד-ים ומנהר עד-אפסי-ארץ
9 Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
לפניו יכרעו ציים ואיביו עפר ילחכו
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali adzabweretsa mitulo kwa iye, mafumu a ku Seba ndi Seba adzapereka mphatso kwa iyeyo.
מלכי תרשיש ואיים מנחה ישיבו מלכי שבא וסבא אשכר יקריבו
11 Mafumu onse adzamuweramira ndipo mitundu yonse idzamutumikira.
וישתחוו-לו כל-מלכים כל-גוים יעבדוהו
12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
כי-יציל אביון משוע ועני ואין-עזר לו
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
יחס על-דל ואביון ונפשות אביונים יושיע
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.
מתוך ומחמס יגאל נפשם וייקר דמם בעיניו
15 Iye akhale ndi moyo wautali; golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye. Anthu amupempherere nthawi zonse ndi kumudalitsa tsiku lonse.
ויחי-- ויתן-לו מזהב שבא ויתפלל בעדו תמיד כל-היום יברכנהו
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse; pamwamba pa mapiri pakhale tirigu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni; zichuluke ngati udzu wakuthengo
יהי פסת-בר בארץ-- בראש הרים ירעש כלבנון פריו ויציצו מעיר כעשב הארץ
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
יהי שמו לעולם-- לפני-שמש ינין (ינון) שמו ויתברכו בו כל-גוים יאשרוהו
18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
ברוך יהוה אלהים--אלהי ישראל עשה נפלאות לבדו
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni.
וברוך שם כבודו-- לעולם וימלא כבודו את-כל הארץ-- אמן ואמן
20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.
כלו תפלות-- דוד בן-ישי

< Masalimo 72 >