< Masalimo 7 >

1 Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini. Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu; pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
שִׁגָּיוֹן לְדָוִד אֲשֶׁר־שָׁר לַֽיהֹוָה עַל־דִּבְרֵי־כוּשׁ בֶּן־יְמִינִֽי׃ יְהֹוָה אֱלֹהַי בְּךָ חָסִיתִי הוֹשִׁיעֵנִי מִכׇּל־רֹדְפַי וְהַצִּילֵֽנִי׃
2 mwina angandikadzule ngati mkango, ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.
פֶּן־יִטְרֹף כְּאַרְיֵה נַפְשִׁי פֹּרֵק וְאֵין מַצִּֽיל׃
3 Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,
יְהֹוָה אֱלֹהַי אִם־עָשִׂיתִי זֹאת אִֽם־יֶשׁ־עָוֶל בְּכַפָּֽי׃
4 ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere, kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,
אִם־גָּמַלְתִּי שֽׁוֹלְמִי רָע וָאֲחַלְּצָה צֽוֹרְרִי רֵיקָֽם׃
5 pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira, lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi ndipo mundigoneke pa fumbi. (Sela)
יִרַדֹּֽף־אוֹיֵב ׀ נַפְשִׁי וְיַשֵּׂג וְיִרְמֹס לָאָרֶץ חַיָּי וּכְבוֹדִי ׀ לֶעָפָר יַשְׁכֵּן סֶֽלָה׃
6 Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu; nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga. Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.
קוּמָה יְהֹוָה ׀ בְּאַפֶּךָ הִנָּשֵׂא בְּעַבְרוֹת צוֹרְרָי וְעוּרָה אֵלַי מִשְׁפָּט צִוִּֽיתָ׃
7 Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani. Alamulireni muli kumwambako;
וַעֲדַת לְאֻמִּים תְּסֽוֹבְבֶךָּ וְעָלֶיהָ לַמָּרוֹם שֽׁוּבָה׃
8 Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo. Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa, monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.
יְהֹוָה יָדִין עַמִּים שׇׁפְטֵנִי יְהֹוָה כְּצִדְקִי וּכְתֻמִּי עָלָֽי׃
9 Inu Mulungu wolungama, amene mumasanthula maganizo ndi mitima, thetsani chiwawa cha anthu oyipa ndipo wolungama akhale motetezedwa.
יִגְמׇר־נָא רַע ׀ רְשָׁעִים וּתְכוֹנֵן צַדִּיק וּבֹחֵן לִבּוֹת וּכְלָיוֹת אֱלֹהִים צַדִּֽיק׃
10 Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba, amene amapulumutsa olungama mtima.
מָגִנִּי עַל־אֱלֹהִים מוֹשִׁיעַ יִשְׁרֵי־לֵֽב׃
11 Mulungu amaweruza molungama, Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.
אֱלֹהִים שׁוֹפֵט צַדִּיק וְאֵל זֹעֵם בְּכׇל־יֽוֹם׃
12 Ngati munthu satembenuka, Mulungu adzanola lupanga lake, Iye adzawerama ndi kukoka uta.
אִם־לֹא יָשׁוּב חַרְבּוֹ יִלְטוֹשׁ קַשְׁתּוֹ דָרַךְ וַֽיְכוֹנְנֶֽהָ׃
13 Mulungu wakonza zida zake zoopsa; Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.
וְלוֹ הֵכִין כְּלֵי־מָוֶת חִצָּיו לְֽדֹלְקִים יִפְעָֽל׃
14 Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse. Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.
הִנֵּה יְחַבֶּל־אָוֶן וְהָרָה עָמָל וְיָלַד שָֽׁקֶר׃
15 Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.
בּוֹר כָּרָה וַֽיַּחְפְּרֵהוּ וַיִּפֹּל בְּשַׁחַת יִפְעָֽל׃
16 Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini; chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.
יָשׁוּב עֲמָלוֹ בְרֹאשׁוֹ וְעַל קׇדְקֳדוֹ חֲמָסוֹ יֵרֵֽד׃
17 Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake; ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.
אוֹדֶה יְהֹוָה כְּצִדְקוֹ וַאֲזַמְּרָה שֵֽׁם־יְהֹוָה עֶלְיֽוֹן׃

< Masalimo 7 >