< Masalimo 68 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane; adani ake athawe pamaso pake.
למנצח לדוד מזמור שיר ב יקום אלהים יפוצו אויביו וינוסו משנאיו מפניו
2 Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali. Monga phula limasungunukira pa moto, oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
כהנדף עשן תנדף כהמס דונג מפני-אש-- יאבדו רשעים מפני אלהים
3 Koma olungama asangalale ndi kukondwera pamaso pa Mulungu; iwo akondwere ndi kusangalala.
וצדיקים--ישמחו יעלצו לפני אלהים וישישו בשמחה
4 Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando, mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo; dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
שירו לאלהים-- זמרו שמו סלו לרכב בערבות--ביה שמו ועלזו לפניו
5 Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
אבי יתומים ודין אלמנות-- אלהים במעון קדשו
6 Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja, amatsogolera amʼndende ndi kuyimba; koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
אלהים מושיב יחידים ביתה-- מוציא אסירים בכושרות אך סוררים שכנו צחיחה
7 Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu, pamene munayenda kudutsa chipululu,
אלהים--בצאתך לפני עמך בצעדך בישימון סלה
8 dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula, pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai. Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
ארץ רעשה אף-שמים נטפו-- מפני אלהים זה סיני-- מפני אלהים אלהי ישראל
9 Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu; munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
גשם נדבות תניף אלהים נחלתך ונלאה אתה כוננתה
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
חיתך ישבו-בה תכין בטובתך לעני אלהים
11 Ambuye analengeza mawu, ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
אדני יתן-אמר המבשרות צבא רב
12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro; mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
מלכי צבאות ידדון ידדון ונות-בית תחלק שלל
13 Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto, mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva, nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
אם-תשכבון בין שפתים כנפי יונה נחפה בכסף ואברותיה בירקרק חרוץ
14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko, zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.
בפרש שדי מלכים בה-- תשלג בצלמון
15 Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero; mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
הר-אלהים הר-בשן הר גבננים הר-בשן
16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri, pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira, kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
למה תרצדון-- הרים גבננים ההר--חמד אלהים לשבתו אף-יהוה ישכן לנצח
17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka, ndi miyandamiyanda; Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
רכב אלהים רבתים אלפי שנאן אדני בם סיני בקדש
18 Pamene Inu munakwera mmwamba, munatsogolera a mʼndende ambiri; munalandira mphatso kuchokera kwa anthu, ngakhale kuchokera kwa owukira, kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.
עלית למרום שבית שבי-- לקחת מתנות באדם ואף סוררים לשכן יה אלהים
19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
ברוך אדני יום יום יעמס-לנו--האל ישועתנו סלה
20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa; Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.
האל לנו אל למושעות וליהוה אדני--למות תצאות
21 Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake, zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
אך-אלהים--ימחץ ראש איביו קדקד שער--מתהלך באשמיו
22 Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani; ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
אמר אדני מבשן אשיב אשיב ממצלות ים
23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu, pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”
למען תמחץ רגלך--בדם לשון כלביך--מאיבים מנהו
24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu; mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
ראו הליכותיך אלהים הליכות אלי מלכי בקדש
25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo; pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
קדמו שרים אחר נגנים בתוך עלמות תופפות
26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu; tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
במקהלות ברכו אלהים אדני ממקור ישראל
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera, pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda, ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.
שם בנימן צעיר רדם--שרי יהודה רגמתם שרי זבלון שרי נפתלי
28 Kungani mphamvu zanu Mulungu; tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
צוה אלהיך עזך עוזה אלהים--זו פעלת לנו
29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu, mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
מהיכלך על-ירושלם-- לך יובילו מלכים שי
30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango, gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu. Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva. Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
גער חית קנה עדת אבירים בעגלי עמים-- מתרפס ברצי-כסף בזר עמים קרבות יחפצו
31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto; Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
יאתיו חשמנים מני מצרים כוש תריץ ידיו לאלהים
32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi imbirani Ambuye matamando. (Sela)
ממלכות הארץ שירו לאלהים זמרו אדני סלה
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba amene amabangula ndi mawu amphamvu.
לרכב בשמי שמי-קדם-- הן יתן בקולו קול עז
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu, amene ulemerero wake uli pa Israeli amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
תנו עז לאלהים על-ישראל גאותו ועזו בשחקים
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika; Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake. Matamando akhale kwa Mulungu!
נורא אלהים ממקדשיך אל ישראל-- הוא נתן עז ותעצמות לעם ברוך אלהים

< Masalimo 68 >