< Masalimo 67 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire.
For the Leader; with string-music. A Psalm, a Song. God be gracious unto us, and bless us; may He cause His face to shine toward us; (Selah)
2 Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.
That Thy way may be known upon earth, Thy salvation among all nations.
3 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Let the peoples give thanks unto Thee, O God; let the peoples give thanks unto Thee, all of them.
4 Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
O let the nations be glad and sing for joy; for Thou wilt judge the peoples with equity, and lead the nations upon earth. (Selah)
5 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Let the peoples give thanks unto Thee, O God; let the peoples give thanks unto Thee, all of them.
6 Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu.
The earth hath yielded her increase; may God, our own God, bless us.
7 Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.
May God bless us; and let all the ends of the earth fear Him.