< Masalimo 66 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo. Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
Make a joyful noise to God, all the earth.
2 Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
Sing forth the glory of his name. Make his praise glorious.
3 Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
Say to God, How awesome are thy works! Through the greatness of thy power thine enemies shall submit themselves to thee.
4 Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” (Sela)
All the earth shall worship thee, and shall sing to thee. They shall sing to thy name. (Selah)
5 Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
Come, and see the works of God, awesome in actions toward the sons of men.
6 Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
He turned the sea into dry land. They went through the river on foot. There we rejoiced in him.
7 Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.
He rules by his might forever. His eyes observe the nations. Let not the rebellious exalt themselves. (Selah)
8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
O bless our God, ye peoples, and make the voice of his praise to be heard,
9 Iye watchinjiriza miyoyo yathu ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
who holds our soul in life, and does not allow our feet to be moved.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva.
For thou, O God, have proved us. Thou have tried us as silver is tried.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
Thou brought us into the net. Thou laid a great burden upon our loins.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu; ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi, koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
Thou caused men to ride over our heads. We went through fire and through water. But thou brought us out into a wealthy place.
13 Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
I will come into thy house with burnt offerings. I will pay thee my vows,
14 Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
which my lips uttered, and my mouth spoke, when I was in distress.
15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. (Sela)
I will offer to thee burnt offerings of fatlings, with the incense of rams. I will offer bullocks with goats. (Selah)
16 Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
Come, and hear, all ye who fear God, and I will declare what he has done for my soul.
17 Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga.
I cried to him with my mouth, and he was extolled with my tongue.
18 Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera;
If I regard iniquity in my heart, the Lord will not hear.
19 koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
But truly God has heard. He has attended to the voice of my prayer.
20 Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine!
Blessed be God, who has not turned away my prayer, nor his loving kindness from me.

< Masalimo 66 >