< Masalimo 65 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo. Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni; kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
Au maître de chant. Psaume de David. Cantique. A toi est due la louange, ô Dieu, dans Sion; c'est en ton honneur qu'on accomplit les vœux.
2 Inu amene mumamva pemphero, kwa inu anthu onse adzafika.
O toi, qui écoutes la prière, tous les hommes viennent à toi.
3 Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo, Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
Un amas d'iniquités pesait sur moi: tu pardonnes nos transgressions.
4 Odala iwo amene inu muwasankha ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu! Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu, za mʼNyumba yanu yoyera.
Heureux celui que tu choisis et que tu rapproches de toi, pour qu'il habite dans tes parvis! Puissions-nous être rassasiés des biens de ta maison, de ton saint temple!
5 Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
Par des prodiges, tu nous exauces dans ta justice, Dieu de notre salut, espoir des extrémités de la terre, et des mers lointaines.
6 amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu, mutadziveka nokha ndi mphamvu.
— Il affermit les montagnes par sa force, il est ceint de sa puissance;
7 Amene munakhalitsa bata nyanja kukokoma kwa mafunde ake, ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
il apaise la fureur des mers, la fureur de leurs flots, et le tumulte des peuples. —
8 Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu; kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera. Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
Les habitants des pays lointains craignent devant tes prodiges, tu réjouis les extrémités, l'Orient et l'Occident.
9 Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira; Inuyo mumalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi kuti upereke tirigu kwa anthu, pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
Tu as visité la terre pour lui donner l'abondance, tu la combles de richesses; la source divine est remplie d'eau: tu prépares le blé, quand tu la fertilises ainsi.
10 Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake, mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
Arrosant ses sillons, aplanissant ses mottes, tu l'amollis par des ondées, tu bénis ses germes.
11 Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka, ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
Tu couronnes l'année de tes bienfaits, sur tes pas ruisselle la graisse.
12 Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira; mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
Les pâturages du désert sont abreuvés, et les collines se revêtent d'allégresse.
13 Madambo akutidwa ndi zoweta ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu; izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.
Les prairies se couvrent de troupeaux, et les vallées se parent d'épis; tout se réjouit et chante.