< Masalimo 63 >
1 Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.
A PSALM OF DAVID, IN HIS BEING IN THE WILDERNESS OF JUDAH. O God, You [are] my God, earnestly I seek You, My soul has thirsted for You, My flesh has longed for You, In a dry and weary land, without waters.
2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
So I have seen You in the sanctuary, To behold Your strength and Your glory.
3 Chifukwa chikondi chanu ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
Because better [is] Your kindness than life, My lips praise You.
4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga, ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
So I bless You in my life, I lift up my hands in Your Name.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona. Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.
As [with] milk and fatness is my soul satisfied, And [with] singing lips my mouth praises.
6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
If I have remembered You on my bed, I meditate on You in the watches.
7 Chifukwa ndinu thandizo langa, ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
For You have been a help to me, And I sing in the shadow of Your wings.
8 Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.
My soul has cleaved after You, Your right hand has taken hold on me.
9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
And they who seek my soul for desolation, Go into the lower parts of the earth.
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.
They cause him to run on the edge of the sword, They are a portion for foxes.
11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo, koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.
And the king rejoices in God, Everyone swearing by Him boasts, But the mouth of those speaking lies is stopped!