< Masalimo 61 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe. Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu; mvetserani pemphero langa.
לַמְנַצֵּחַ ׀ עַֽל־נְגִינַת לְדָוִֽד׃ שִׁמְעָה אֱלֹהִים רִנָּתִי הַקְשִׁיבָה תְּפִלָּתִֽי׃
2 Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka; tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
מִקְצֵה הָאָרֶץ ׀ אֵלֶיךָ אֶקְרָא בַּעֲטֹף לִבִּי בְּצוּר־יָרוּם מִמֶּנִּי תַנְחֵֽנִי׃
3 Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga, nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.
כִּֽי־הָיִיתָ מַחְסֶה לִי מִגְדַּל־עֹז מִפְּנֵי אוֹיֵֽב׃
4 Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
אָגוּרָה בְאׇהׇלְךָ עוֹלָמִים אֶחֱסֶה בְסֵתֶר כְּנָפֶיךָ סֶּֽלָה׃
5 Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga; mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.
כִּֽי־אַתָּה אֱלֹהִים שָׁמַעְתָּ לִנְדָרָי נָתַתָּ יְרֻשַּׁת יִרְאֵי שְׁמֶֽךָ׃
6 Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu, zaka zake kwa mibado yochuluka.
יָמִים עַל־יְמֵי־מֶלֶךְ תּוֹסִיף שְׁנוֹתָיו כְּמוֹ־דֹר וָדֹֽר׃
7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya; ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.
יֵשֵׁב עוֹלָם לִפְנֵי אֱלֹהִים חֶסֶד וֶאֱמֶת מַן יִנְצְרֻֽהוּ׃
8 Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.
כֵּן אֲזַמְּרָה שִׁמְךָ לָעַד לְֽשַׁלְּמִי נְדָרַי יוֹם ׀ יֽוֹם׃

< Masalimo 61 >