< Masalimo 6 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide. Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu.
למנצח בנגינות על השמינית מזמור לדוד יהוה אל באפך תוכיחני ואל בחמתך תיסרני׃
2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
חנני יהוה כי אמלל אני רפאני יהוה כי נבהלו עצמי׃
3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
ונפשי נבהלה מאד ואת יהוה עד מתי׃
4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
שובה יהוה חלצה נפשי הושיעני למען חסדך׃
5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda? (Sheol h7585)
כי אין במות זכרך בשאול מי יודה לך׃ (Sheol h7585)
6 Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
יגעתי באנחתי אשחה בכל לילה מטתי בדמעתי ערשי אמסה׃
7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
עששה מכעס עיני עתקה בכל צוררי׃
8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
סורו ממני כל פעלי און כי שמע יהוה קול בכיי׃
9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa.
שמע יהוה תחנתי יהוה תפלתי יקח׃
10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.
יבשו ויבהלו מאד כל איבי ישבו יבשו רגע׃

< Masalimo 6 >