< Masalimo 59 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Pamene Sauli anatumiza anthu kuti akalondere nyumba ya Davide ndi cholinga choti amuphe. Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu; munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.
達味金詩,交與樂官。調寄「莫要毀壞」。 我主,求你由我的仇敵中,救我免難,求你從攻擊我者中,使戈脫險;
2 Landitseni kwa anthu ochita zoyipa ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.
求你救我脫離為非作歹的人,求你救我脫離好流人血的人。
3 Onani momwe iwo akundibisalira! Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane; osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.
上主,你看,我雖然沒有作過惡,沒有犯過罪,但強橫人為害我的性命,卻群起與我作對。
4 Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo. Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!
我雖然無辜,他們卻跑來挑戰,求你醒來扶助我,且予以察看。
5 Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse; musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.
因為你是上主,萬軍的天主,以色列的天主,醒來嚴罰這些群眾,別恩待這些背信的惡徒。
6 Iwo amabweranso madzulo akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyendayenda mu mzinda.
他們晚上歸來,狂吠如犬,他們環繞城池,四周圍轉。
7 Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo; iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo, ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”
看,他們的唇舌宛如利劍,且滿口傲慢說:有誰聽見?
8 Koma Inu Yehova, mumawaseka, mumayinyoza mitundu yonseyo.
但是你,上主,你必嘲笑他們,你必譏諷這般異民。
9 Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa.
我的力量,我只有仰望於你,因為你是天主,是我的堡壘。
10 Mulungu wanga wachikondi. Mulungu adzapita patsogolo panga ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.
願那愛我的天主援助我,使我因仇敵失敗而歡樂!
11 Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu, kuopa kuti anthu anga angayiwale. Mwa mphamvu zanu, lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.
天主,求你擊殺他們,免得侵犯我的人民;上主,我的謢盾,你以強力制服他們。
12 Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo chifukwa cha mawu a milomo yawo, iwo akodwe mʼkunyada kwawo. Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula
他們口唇所說的話語:就是他們口舌的罪過,他們因自己的驕傲咒罵與謊言,自陷網羅!
13 muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo.
求你發怒滅絕他們,滅絕他們無一存立,使人知道:天主在雅各伯為王直達地極。
14 Iwo amabweranso madzulo, akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyenda mu mzinda.
他們晚上歸來,狂吠如犬,他們環繞城池,四周圍轉。
15 Iwo amayendayenda kufuna chakudya ndipo amawuwa ngati sanakhute.
他們到處遊蕩,覓食餬口。若不得飽食,便狂吠不休。
16 Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu, mmawa ndidzayimba zachikondi chanu; pakuti ndinu linga langa, pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.
但是我要稱你的威能,每日清晨歡呼你的寬仁,因為只有你是我的碉堡,是我困厄時日的避難所。
17 Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.
我的力量,我只有向你歡唱,因為只有你是天主,是我的保障。你是我的天主,你對我慈祥。