< Masalimo 57 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo, pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo. Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu mpaka chiwonongeko chitapita.
In finem, Ne disperdas, David in tituli inscriptionem, cum fugeret a facie Saul in speluncam. Miserere mei Deus, miserere mei: quoniam in te confidit anima mea. Et in umbra alarum tuarum sperabo, donec transeat iniquitas.
2 Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba, kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
Clamabo ad Deum altissimum: Deum qui benefecit mihi.
3 Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa, kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri. Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.
Misit de cælo, et liberavit me: dedit in opprobrium conculcantes me. Misit Deus misericordiam suam, et veritatem suam,
4 Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa.
et eripuit animam meam de medio catulorum leonum: dormivi conturbatus. Filii hominum dentes eorum arma et sagittæ: et lingua eorum gladius acutus.
5 Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba; mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
Exaltare super cælos Deus: et in omnem terram gloria tua.
6 Iwo anatchera mapazi anga ukonde ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa. Anakumba dzenje mʼnjira yanga koma agweramo okha mʼmenemo.
Laqueum paraverunt pedibus meis: et incurvaverunt animam meam. Foderunt ante faciem meam foveam: et inciderunt in eam.
7 Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu mtima wanga ndi wokhazikika. Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
Paratum cor meum Deus, paratum cor meum: cantabo, et psalmum dicam.
8 Dzuka moyo wanga! Dzukani zeze ndi pangwe! Ndidzadzuka mʼbandakucha.
Exurge gloria mea, exurge psalterium et cithara: exurgam diluculo.
9 Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.
Confitebor tibi in populis Domine: et psalmum dicam tibi in gentibus:
10 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba; kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.
Quoniam magnificata est usque ad cælos misericordia tua, et usque ad nubes veritas tua.
11 Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba, mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
Exaltare super cælos Deus: et super omnem terram gloria tua.

< Masalimo 57 >