< Masalimo 55 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe. Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu, musakufulatire kupempha kwanga,
TO THE OVERSEER. WITH STRINGED INSTRUMENTS. AN INSTRUCTION OF DAVID. Give ear, O God, [to] my prayer, And do not hide from my supplication.
2 mverani ndipo mundiyankhe. Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru
Attend to me, and answer me, I mourn in my (meditation) and make a noise,
3 chifukwa cha mawu a adani anga, chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa; pakuti andidzetsera masautso ndipo akundizunza mu mkwiyo wawo.
Because of the voice of an enemy, Because of the oppression of the wicked, For they cause sorrow to move against me, And in anger they hate me.
4 Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga; mantha a imfa andigwera.
My heart is pained within me, And terrors of death have fallen on me.
5 Mantha ndi kunjenjemera zandizinga; mantha aakulu andithetsa nzeru.
Fear and trembling come to me, And horror covers me.
6 Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda! Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.
And I say, “Who gives to me a pinion as a dove?” I fly away and rest,
7 Ndikanathawira kutali ndi kukakhala mʼchipululu.
Behold, I move far off, I lodge in a wilderness. (Selah)
8 Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo; kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”
I hurry escape for myself, From a rushing wind, from a whirlwind.
9 Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo; pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.
Swallow up, O Lord, divide their tongue, For I saw violence and strife in a city.
10 Usana ndi usiku iwo akuzungulirazungulira pa makoma ake; nkhwidzi ndi kuzunza kuli mʼkati mwake.
By day and by night they go around it, on its walls. Both iniquity and perverseness [are] in its midst,
11 Mphamvu zowononga zili pa ntchito mu mzinda; kuopseza ndi mabodza sizichoka mʼmisewu yake.
Mischiefs [are] in its midst. Fraud and deceit do not depart from its street.
12 Akanakhala mdani akundinyoza, ine ndikanapirira; akanakhala mdani akudzikweza yekha kutsutsana nane, ndikanakabisala.
For an enemy does not reproach me, or I bear [it], He who is hating me Has not magnified himself against me, Or I hide from him.
13 Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.
But you, a man—as my equal, My familiar friend, and my acquaintance.
14 Mnzanga amene nthawi ina tinkasangalala pa chiyanjano chokoma ku nyumba ya Mulungu.
When together we sweeten counsel, We walk into the house of God in company.
15 Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi; alowe mʼmanda ali amoyo pakuti choyipa chili pakati pawo. (Sheol )
Desolations [are] on them, They go down [to] Sheol—alive, For wickedness [is] in their dwelling, in their midst. (Sheol )
16 Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu, ndipo Yehova anandipulumutsa.
I call to God, and YHWH saves me.
17 Madzulo, mmawa ndi masana ndimalira mowawidwa mtima, ndipo Iye amamva mawu anga.
Evening, and morning, and noon, I meditate, and make a noise, and He hears my voice,
18 Iye amandiwombola ine osavulazidwa pa nkhondo imene yafika kulimbana nane, ngakhale kuti ndi ambiri amene akunditsutsa.
He has ransomed my soul in peace From him who is near to me, For with the multitude they were with me.
19 Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya, adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga, chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa ndipo saopa Mulungu.
God hears and afflicts them, And He sits of old. (Selah) Because they have no changes, and do not fear God,
20 Mnzanga woyenda naye wathira nkhondo abwenzi ake; iye akuphwanya pangano ake.
He has sent forth his hands against his well-wishers, He has defiled his covenant.
21 Mawu ake ndi osalala kuposa batala komabe nkhondo ili mu mtima mwake; mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta, komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.
His mouth has been sweeter than honey, And his heart [is] war! His words have been softer than oil, And they [are] drawn [swords].
22 Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.
Cast on YHWH that which He has given you, And He sustains you, He does not permit the moving of the righteous forever.
23 Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa kulowa mʼdzenje lachiwonongeko; anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo sadzakhala moyo theka la masiku awo, koma ine ndimadalira Inu.
And You, O God, bring them down To a pit of destruction, Men of blood and deceit do not reach to half their days, And I trust in You!