< Masalimo 54 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.” Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
達味訓誨歌,交與樂官,和以絃樂。 作於齊弗人來對撒烏耳說:「看,達味藏在我們這裡」時。 天主,求你因你的名賜我救援,求你並以你的權能為我伸冤。
2 Imvani pemphero langa, Inu Mulungu mvetserani mawu a pakamwa panga.
天主,求你俯聽我的祈求,側耳傾聽我的投訴。
3 Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu.
傲慢的人起來向我進攻,蠻橫的人想謀害我的生命,他們沒有把天主放在眼中。(休止)
4 Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.
請看,天主必定給我助陣,上主必扶持我生命。
5 Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe; mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.
求你使災禍報應在我的仇讎身上,求你憑你的忠誠將他們消除滅亡。
6 Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino.
我要自願向上主祭獻;上主,我要對你的美名稱讚。
7 Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse, ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.
因為你救我脫離了一切災難,使我親眼看見我的仇敵潰散。

< Masalimo 54 >