< Masalimo 53 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.
To him that excelleth on Mahalath. A Psalme of David to give instruction. The foole hath saide in his heart, There is no God. they haue corrupted and done abominable wickednes: there is none that doeth good.
2 Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano pa ana a anthu kuti aone ngati alipo wina wanzeru, wofunafuna Mulungu.
God looked downe from heauen vpon the children of men, to see if there were any that would vnderstand, and seeke God.
3 Aliyense wabwerera, iwo onse pamodzi akhala oyipa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino, ngakhale mmodzi.
Euery one is gone backe: they are altogether corrupt: there is none that doth good, no not one.
4 Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi; anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi, ndipo sapemphera kwa Mulungu?
Doe not the workers of iniquitie knowe that they eate vp my people as they eate bread? they call not vpon God.
5 Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.
There they were afraide for feare, where no feare was: for God hath scattered the bones of him that besieged thee: thou hast put them to confusion, because God hath cast them off.
6 Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni! Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake, lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!
Oh giue saluation vnto Israel out of Zion: when God turneth the captiuitie of his people, then Iaakob shall reioyce, and Israel shalbe glad.