< Masalimo 52 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.” Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu? Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse, iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?
למנצח משכיל לדוד ב בבוא דואג האדמי-- ויגד לשאול ויאמר לו-- בא דוד אל-בית אחימלך ג מה-תתהלל ברעה הגבור חסד אל כל-היום
2 Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena; lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nʼkunyenga.
הוות תחשב לשונך כתער מלטש עשה רמיה
3 Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi. Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. (Sela)
אהבת רע מטוב שקר מדבר צדק סלה
4 Umakonda mawu onse opweteka, iwe lilime lachinyengo!
אהבת כל-דברי-בלע לשון מרמה
5 Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya: iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako; iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.
גם-אל יתצך לנצח יחתך ויסחך מאהל ושרשך מארץ חיים סלה
6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha; adzamuseka nʼkumanena kuti,
ויראו צדיקים וייראו ועליו ישחקו
7 “Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!”
הנה הגבר-- לא ישים אלהים מעוזו ויבטח ברב עשרו יעז בהותו
8 Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu; ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu kwa nthawi za nthawi.
ואני כזית רענן-- בבית אלהים בטחתי בחסד-אלהים עולם ועד
9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.
אודך לעולם כי עשית ואקוה שמך כי-טוב נגד חסידיך

< Masalimo 52 >