< Masalimo 51 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.
2 Munditsuke zolakwa zanga zonse ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.
3 Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
4 Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa ndipo ndachita zoyipa pamaso panu, Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
5 Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa, wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
6 Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga; mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.
7 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera, munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
8 Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo, mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
9 Mufulatire machimo anga ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.
10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.
13 Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.
14 Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu wa chipulumutso changa, ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.
15 Inu Ambuye tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.
16 Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba. Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.
17 Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka; mtima wosweka ndi wachisoni Inu Mulungu simudzawunyoza.
18 Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere; mumange makoma a Yerusalemu.
19 Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo, nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu; ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.