< Masalimo 5 >
1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide. Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova, ganizirani za kusisima kwanga
2 Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
3 Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo.
4 Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa; choyipa sichikhala pamaso panu.
5 Onyada sangathe kuyima pamaso panu; Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.
6 Mumawononga iwo amene amanena mabodza; anthu akupha ndi achinyengo, Yehova amanyansidwa nawo.
7 Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu, ndidzalowa mʼNyumba yanu; mwa ulemu ndidzaweramira pansi kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
8 Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu chifukwa cha adani anga ndipo wongolani njira yanu pamaso panga.
9 Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike; mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko. Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.
10 Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu! Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo. Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri, pakuti awukira Inu.
11 Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
12 Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama; mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.